Zephaniah 3:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale kutali kutsidya kwa mitsinje ya ku Etiopiya, anthu ondipembedza, anthu anga obalalika, adzapereka nsembe kwa Ine.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuchokera tsidya lija la mitsinje ya Kusi ondipembedza, ndiwo mwana wamkazi wa obalalika anga, adzabwera nacho chopereka changa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuchokera kutsidya kwa mitsinje ya ku Kusi anthu anga ondipembedza, omwazikana, adzandibweretsera zopereka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kucokera tsidya lija la mitsinje ya Kusi ondipembedza, ndiwo mwana wamkazi wa obalalika anga, adzabwera naco copereka canga.