Zephaniah 3:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo ndidzaŵakhaulitsa onse amene amakuzunzani. Ndidzapulumutsa otayika ndi kusonkhanitsa onse obalalika. Ndidzaŵatamanda ndi kuŵapatsa ulemu, kulikonse kumene adani ao ankaŵachititsa manyazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, nthawi yomweyo ndidzachita nao onse akuzunza iwe; ndipo ndidzapulumutsa wotsimphinayo, ndi kusonkhanitsa wopirikitsidwayo; ndipo ndidzawaika akhale chilemekezo ndi dzina, iwo amene manyazi ao anali m'dziko lonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani, nthawi imeneyo ndidzathana ndi onse amene anakuponderezani; ndidzapulumutsa olumala ndi kusonkhanitsa amene anamwazika. Ndidzawayamikira ndi kuwachitira ulemu mʼdziko lililonse mmene anachititsidwa manyazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, nthawi yomweyo ndidzacita nao onse akuzunza iwe; ndipo ndidzapulumutsa wotsimphinayo, ndi kusonkhanitsa wopitikitsidwayo; ndipo ndidzawaika akhale cilemekezo ndi dzina, iwo amene manyazi ao anali m'dziko lonse.