Zephaniah 3:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti, “Ndaononga mitundu yonse ya anthu ndipo malinga ao onse ankhondo ndaŵaphwasula. Miseu yao ndaifafaniza palibenso anthu oyendamo. Mizinda yao yachitika bwinja, mulibe munthu ndi mmodzi yemwe wotsalamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndaononga amitundu; nsanja zao za kungodya nza bwinja, ndapasula miseu yao, palibe wopitapo; midzi yao yaonongeka, palibe munthu, palibe wokhalamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndachotseratu mitundu ya anthu; ndagwetsa malinga awo. Ndipo sindinasiye ndi mmodzi yemwe mʼmisewu mwawo, popanda aliyense wodutsa. Mizinda yawo yawonongedwa; palibe aliyense adzatsalemo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndaononga amitundu; nsanja zao za kungondya nza bwinja, ndapasula miseu yao, palibe wopitapo; midzi yao yaonongeka, palibe munthu, palibe wokhalamo.