Zephaniah 3:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidaaganiza kuti ndithudi anthu anga andiwopa, kuti avomera malango anga, ndipo kuti saiŵala malamulo anga. Koma ndi pamene iwo adanyanyira kumachita zoipa pa zochita zao zonse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinati, Zedi udzandiopa Ine, udzalola kulangizidwa, kuti pokhala pake pasaonongeke, monga mwa zonse ndamuikira; koma analawirira mamawa, navunditsa machitidwe ao onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinati, ‘Ndithudi, anthu a mu mzindawu adzandiopa ndi kumvera kudzudzula kwanga!’ Ndipo sindidzawononga nyumba zawo, kapena kuwalanganso. Koma iwo anali okonzeka kuchita mwachinyengo zinthu zonse zimene amachita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinati, Zedi udzandiopa Ine, udzalola kulangizidwa, kuti pokhala pace pasaonongeke, monga mwa zonse ndamuikira; koma analawirira mamawa, nabvunditsa macitidwe ao onse.