bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
1 Corinthians 4
1 Corinthians 4
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 5 →
1
Cotero munthu atiyese ife, monga atumiki a Kristu, ndi adindo a zinsinsi za Mulungu.
2
Komatu pano pafunika za adindo, kuti munthu akhale wokhulupirika.
3
Koma kwa ine kuli kanthu kakang'ono ndithu, kuti ndiweruzidwe ndi Inu, kapena pa bwalo la munthu; koma sindiweruza ngakhale ndekha.
4
Pakuti sindidziwa kanthu kakundiparamulitsa; koma m'menemo sindiyesedwa wolungama; koma wondiweruza ine ndiye Ambuye.
5
Cifukwa cace musaweruze kanthu isanadze nthawi yace, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wace wa kwa Mulungu.
6
Koma izi, abale, ndadziphiphiritsira ndekha ndi Apolo, cifukwa ca inu, kuti mwa ife mukaphunzire kusapitirira zimene zilembedwa; kuti pasakhale mmodzi wodzitukumulira mnzace ndi kukana wina.
7
Pakuti akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli naco ciani cosati wacilandira? Koma ngati wacilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunacilandira?
8
M wadzala kale, mwalemerera kale, mwacita ufumu opanda ife; ndipo mwenzi mucitadi ufumu, kuti ifenso tikacite ufumu pamodzi ndi inu.
9
Pakuti ndiyesa, kuti Mulungu anaoneketsa ife atumwi otsiriza, monga titi tife; pakuti takhala ife coonetsedwa ku dziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu.
10
Tiri opusa ife cifukwa ca Kristu, koma muli ocenjera inu mwa Kristu; tiri ife ofoka, koma inu amphamvu; inu ndinu olemekezeka, koma ife ndife onyozeka.
11
Kufikira nthawi yomwe yino timva njala, timva ludzu, tid amarisece, tikhomedwa, tiribe pokhazikika;
12
ndipo tigwiritsa nchito, ndi kucita ndi manja athu a ife tokha; polalatidwa tidalitsa; pozunzidwa, tipirira;
13
ponamizidwa, tipempha; takhala monga zonyansa za dziko lapansi, litsiro la zinthu zonse, kufikira tsopano,
14
Sindilembera izi kukucititsani manyazi, koma kucenjeza inu monga ana anga okondedwa.
15
Pakuti mungakhale muli nao aphunzitsi zikwi khumi mwa Kristu, mulibe atate ambiri; pakuti mwa Kristu Yesu ine ndinabala Inu mwa Uthenga Wabwino.
16
Cifukwa cace ndikupemphani, khalani akutsanza ine.
17
Cifukwa ca ici ndatuma kwa inu Timoteo, ndiye mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye, amene adzakumbutsa inu njira zanga za mwa Kristu, monga ndiphunzitsa ponsepom'Mipingo yonse.
18
Koma ena adzitukumula, monga ngati sindinalinkudza kwa inu.
19
Koma ndidzafika kwa inu msanga, akandilola Ambuye; ndipo ndidzazindikira si mau a iwo odzitukumula, koma mphamvuyi.
20
Pakuti ufumu wa Mulungu suli m'mau, koma mumphamvu, Mufuna ciani?
21
Kodi ndifike kwa inu ndi ndodo, kapena mwacikondi, ndi mzimu wakufatsa?
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16