bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
1 Timothy 2
1 Timothy 2
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 3 →
1
Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti acitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, cifukwa ca anthu onse;
2
cifukwa ca mafumu ndi onse akucita ulamuliro kuti m'moyo mwathu tikakhale odika mtima, ndi acete m'kulemekeza Mulungu, ndi m'kulemekezeka monse.
3
Pakuti ici ncokoma ndi colandirika pamaso pa Mulungu Mpulumutsi wathu;
4
amene afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira coonadi.
5
Pakuti pali Mulungu mmodzi, ndi Mtetezi mmodzi pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye munthu, Kristu Yesu,
6
amene anadzipereka yekha ciombolom'malo mwa onse; umboni m'nyengo zace;
7
umene anandiika ine mlaliki wace ndi mtumwi (ndinena zoona, wosanama ine), mphunzitsi wa amitundu m'cikhulupiriro ndi coonadi.
8
Cifukwa cace ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera, opanda mkwiyo ndi makani.
9
Momwemonso, akazi adzibveke okha ndi cobvala coyenera, ndi manyazi, ndi cidziletso; osati ndi tsitsi lace loluka, ndi golidi kapena ngale, kapena maraya a mtengo wace wapatali;
10
komatu (umo mokomera akazi akubvomereza kulemekeza Mulungu), mwa nchito zabwino.
11
Mkazi aphunzire akhale wacete m'kumvera konse.
12
Koma sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale cete.
13
Pakuti Adamu anayamba kulengedwa, pamenepo Heva;
14
ndipo Adamu sananyengedwa, koma mkaziyo ponyengedwa analowa m'kulakwa;
15
koma adzapulumutsidwa mwa kubala mwana, ngati akhala m'cikhulupiriro ndi cikondi ndi ciyeretso pamodzi ndi cidziletso.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6