bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Acts 3
Acts 3
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 4 →
1
Koma Petro ndi Yohane analikukwera kunka kuKacisi pa ora lakupembedza, ndilo lacisanu ndi cinai.
2
Ndipo munthu wina wopunduka miyendo cibadwire ananyamulidwa, amene akamuika masiku onse pa khomo la Kacisi lochedwa Lokongola, kuti apemphe zaulere kwa iwo akulowa m'Kacisi;
3
ameneyo, pakuona Petro ndi Yohane akuti alowe m'Kacisi, anapempha alandire caulere.
4
Ndipo Petro, pompenyetsetsa iye pamodzi ndi Yohane, anati, Tiyang'ane ife.
5
Ndipo iye anabvomereza iwo, nalingirira kuti adzalandira kanthu.
6
Koma Petro anati, Siliva ndi golidi ndiribe; koma cimene ndiri naco, ici ndikupatsa, M'dzina la Yesu Kristu Mnazarayo, yenda,
7
Ndipo anamgwira Iye ku dzanja lace lamanja, namnyamutsa; ndipo pomwepo mapazi ace ndi mfundo za kumapazi zinalimbikitsidwa.
8
Ndipo anazunzuka, naimirira, nayenda; ndipo analowa pamodzi nao m'Kacisi, nayenda, nalumpha, nayamika Mulungu.
9
Ndipo anthu onse anamuona iye, alikuyenda ndi kuyamika Mulungu;
10
namzindikira iye, kuti ndiye amene anakhala pa Khomo Lokongola la Kacisi: ndipo anadzazidwa ndi kudabwa ndi kuzizwa pa ici cidamgwera.
11
Koma m'mene anagwira Petro ndi Yohane, anawathamangira pamodzi anthu onse ku khumbi lochedwa la Solomo, alikudabwa ndithu.
12
Koma m'mene Petro anaciona, anayankha kwa anthu, Amuna inu a Israyeli, muzizwa naye bwanji ameneyo? kapena mutipenyetsetsa ife bwanji, monga ngati tamyendetsa iye ndi mphamvu ya ife eni, kapena ndi cipembedzo cathu?
13
Mulungu wa Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, analemekeza Mwana wace Yesu; amene, inu munampereka ndi kumkaniza pa Pilato, poweruza iyeyu kummasula.
14
Koma inu munakaniza Woyera ndi Wolungamayo, ndipo munapempha kuti munthu wambanda apatsidwe kwa inu,
15
ndipo munamupha Mkulu wa moyo; amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa; za ici ife tiri mboni.
16
Ndipo pa cikhulupiriro ca m'dzina lace dzina lacelo linalimbikitsa iye amene mumuona, nimumdziwa; ndipo cikhulupiriro ciri mwa iye cinampatsa kucira konse kumeneku pamaso pa inu nonse.
17
Ndipo tsopano, abale, ndidziwa kuti munacicita mosadziwa, monganso akulu anu.
18
Koma zimene Mulungu analalikiratu m'kamwa mwa aneneri onse, kuti adzamva kuwawa Kristu, iye anakwaniritsa cotero.
19
Cifukwa cace lapani, bwererani kuti afafanizidwe macimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zocokera ku nkhope ya Ambuye;
20
ndipo atume amene anaikidwa kwa inu, Kristu Yesu;
21
amene thambo la kumwamba liyenera kumlandira kufikira nthawi zakukonzanso zinthu zonse, zimene Mulunguanalankhula za izo m'kamwa mwa aneneri ace oyera ciyambire.
22
Mosetu anati, Mbuye Mulungu adzaukitsira inu mneneri mwa abale anu, ngati ine; mudzamvera iye m'zinthu ziri zonse akalankhule nanu.
23
Ndipo kudzali, kuti wamoyo ali yensesamvera mneneri ameneyu, adzasakazidwa konse mwa anthu.
24
Koma angakhale aneneri onse kuyambira Samuelindi akumtsatira, onse amene analankhula analalikira za masiku awa.
25
Inu ndinu ana a aneneri, ndi a panganolo Mulungu anapangana ndi makolo anu ndi kunena kwa Abrahamu, Ndipo mu mbeu yako mafuko onse a dziko adzadalitsidwa.
26
Kuyambira ndi inu, Mulungu, ataukitsa Mwana wace, anamtuma kukudalitsani inu, ndi kukubwezani yense ku zoipa zace.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28