bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Amos 1
Amos 1
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 2 →
1
MAU a Amosi, amene anali mwa oweta ng'ombe a ku Tekoa, ndiwo amene anawaona za Israyeli masiku a Uziya mfumu ya Yuda, ndi masiku a Yerobiamu mwana wa Yoasi mfumu ya Israyeli, zitatsala zaka ziwiri cisanafike cibvomezi.
2
Ndipo anati, Yehova adzadzuma ali m'Ziyoni, nadzamveketsa mau ace ali m'Yerusalemu; podyetsa abusa padzacita cisoni, ndi mutu wa Karimeli udzauma.
3
Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za Damasiko, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza anapuntha Gileadi ndi zopunthira zacitsulo;
4
koma ndidzatumiza moto ku nyumba ya Hazaeli, ndipo udzanyeketsa nyumba zacifumu za Benihadadi.
5
Ndipo ndidzatyola mpiringidzo wa Damasiko, ndi kulikha okhala m'cigwa ca Aveni, ndi iye wogwira ndodo yacifumu m'Betedeni; ndi anthu a Aramu adzalowa ndende ku Kiri, ati Yehova.
6
Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za Gaza, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza anatenga ndende anthu onse kuwapereka kwa Edomu;
7
koma ndidzatumiza moto pa linga la Gaza, ndipo udzatha nyumba zace zacifumu;
8
ndipo ndidzalikha okhala m'Asidodi, ndi iye wogwira ndodo yacifumu m'Asikeloni; ndipo ndidzabwezera Ekroni dzanja langa limlange; ndi Afilisti otsala adzatayika, ati Ambuye Yehova.
9
Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za Turo, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza anapereka anthu onse kwa Edomu, osakumbukila pangano lacibale;
10
koma ndidzatumiza moto pa linga la Turo, ndipo udzanyeketsa nyumba zace zacifumu.
11
Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za Edomu, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza analondola mphwace ndi lupanga, nafetsa cifundo cace conse, ndi mkwiyo wace unang'amba cing'ambire, nasunga mkwiyo wace cisungire;
12
koma ndidzatumiza moto pa Temani, udzanyeketsa nyumba zacifumu za Bozira.
13
Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za ana a Amoni, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza anatumbula akazi ali m'pakati a Gileadi, kuti akuze malire ao;
14
koma ndidzayatsa moto pa linga la Raba, udzanyeketsa nyumba zacifumu zace, ndi kupfuula tsiku la nkhondo, ndi namondwe, tsiku la kabvumvulu;
15
ndipo mfumu yao idzalowa kundende, iyo ndi akalonga ace pamodzi, ati Yehova.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9