bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Haggai 1
Haggai 1
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 2 →
1
CAKA caciwiri ca mfumu Dariyo, mwezi wacisanu ndi cimodzi, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri kwa Zerubabele mwana wa Sealitiyeli, ciwanga ca Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kuti,
2
Atero Yehova wa makamu, akuti, Anthu awa anena, Nthawi siinafike, nthawi yakumanga nyumba ya Yehova.
3
Pamenepo mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti,
4
Kodi imeneyi ndiyo nthawi yakuti inu nokha mukhala m'nyumba zanu zocingidwa m'katimo, ndi nyumba iyi ikhale yopasuka?
5
Cifukwa cace tsono, atero Yehova wa makamu: Mtima wanu usamalire njira zanu.
6
Mwabzala zambiri, koma mututa pang'ono; mukudya, koma osakhuta; mukumwa, koma osakoledwa; mudzibveka, koma palibe wofundidwa; ndi iye wolembedwa nchito yakulipidwa alandirira kulipirako m'thumba lobooka.
7
Atero Yehova wa makamu: Mtima wanu usamalire njira zanu.
8
Kwerani ku dziko la mapiri, ndi kukwera nayo mitengo, nimumange nyumbayi; ndipo kudzandikomera, ndipo ndidzalemekezedwa, ati Yehova.
9
Munayembekezera zambiri, koma taonani, pang'ono; ndipo, mutabwera napo kwanu, ndinauzirapo. Cifukwa ninji? ati Yehova wa makamu. Cifukwa ca nyumba yanga yokhala yopasuka, ndipo nuthamangira yense kunyumba kwace.
10
M'mwemo cifukwa ca inu kumwamba kukaniza mame, ndi nthaka ikaniza zipatso zace.
11
Ndipo ndinaitana cirala cidzere dziko, ndi mapiri, ndi tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi zimene ibala nthaka, ndi anthu, ndi zoweta, ndi nchito zonse za manja.
12
Pamenepo Zerubabele mwana wa Sealitiyeli, ndi Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkuru wa ansembe, ndi otsala onse a anthu, anamvera mau a Yehova Mulungu wao, ndi mau a Hagai mneneri, monga Yehova Mulungu wao adamtuma; ndipo anthu anaopa pamaso pa Yehova.
13
Ndipo Hagai mthenga wa Yehova m'uthenga wa Yehova ananena ndi anthu, ndi kuti, Ine ndiri nanu, ati Yehova.
14
Ndipo Yehova anautsa mzimu wa Zerubabele mwana wa Sealitiyeli, ciwanga ca Yuda, ndi mzimu wa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi mzimu wa otsala onse a anthu, ndipo anadza nagwira nchito m'nyumba ya Yehova wa makamu, Mulungu wao,
15
tsiku la makumi awiri ndi anai la mwezi, mwezi wacisanu ndi cimodzi, caka caciwiri ca mfumu Dariyo.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 2 →
All chapters:
1
2