bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Hebrews 6
Hebrews 6
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 7 →
1
Mwa ici, polekana nao mau a ciyambidwe ca Kristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu; osaikanso maziko a kutembenuka mtima kusiyana nazo nchito zakufa, ndi a cikhulupiriro ca pa Mulungu,
2
a ciphunzitso ca ubatizo, a kuika manja, a kuuka kwa akufa, ndi a ciweruziro cosatha.
3
Ndipo ici tidzacita, akatilola Mulungu.
4
Pakuti sikutheka kuwakonzanso, atembenuke mtima, iwo amene anaunikidwa pa nthawi yace, nalawa mphatso ya Kumwamba, nakhala olandirana naye Mzimu Woyera,
5
nalawa mau okoma a Mulungu, ndi mphamvu ya nthawi irinkudza,
6
koma anagwa m'cisokero; popeza adzipaeikiranso okha Mwana wa Mulungu, namcititsa manyazi poyera.
7
Pakuti nthaka imene idamwa mvula iigwera kawiri kawiri, nipatsa therere loyenera iwo amene adailimira, ilandira dalitso locokera kwa Mulungu:
8
koma ikabala minga ndi mitungwi, itayika; nitsala pang'ono ikadatembereredwa; citsiriziro cace ndico kutenthedwa.
9
Koma, okondedwa, takopeka mtima kuti za inu ziri zoposa ndi zophatikana cipulumutso, tingakhale titero pakulankhula;
10
pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala nchito yanu, ndi cikondico mudacionetsera ku dzina lace, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.
11
Koma tikhumba kuti yense wa inu aonetsere cangu comweci colinga ku ciyembekezo cokwanira kufikira citsiriziro;
12
kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikulowa malonjezano mwa cikhulupiriro ndi kuleza mtima.
13
Pakuti pamene Mulungu analonjezana naye Abrahamu, popeza analibe wamkuru woposa kumlumbira, analumbira pa iye yekha,
14
nati, Kudalitsatu ndidzakudalitsa iwe, ndipo kucurukitsa ndidzakucurukitsa iwe.
15
Ndipo potero atapirira analandira lonjezanolo.
16
Pakuti anthu amalumbira pa wamkulu; ndipo m'citsutsano cao ciri conse lumbiro litsiriza kutsimikiza.
17
Momwemo Mulungu, pofuna kuonetsera mocurukira kwa olowa a lonjezano kuti cifuniro cace sicisinthika, analowa pakati ndi lumbiro;
18
kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sakhoza kunama, tikakhale naco coticenjeza colimba, ife amene tidathawira kucigwira ciyembekezo coikika pamaso pathu;
19
cimene tiri naco ngati nangula wa moyo, cokhazikika ndi colimbanso, ndi cakulowa m'katikati mwa cophimba;
20
m'mene Yesu mtsogoleri analowamo cifukwa ca ife, atakhala mkulu wa ansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melikizedeke.
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13