bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
John 20
John 20
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 21 →
1
Koma tsiku loyamba la Sabata anadza Mariya wa Magadala mamawa, kusanayambe kuca, kumanda, napenya mwala wocotsedwa kumanda.
2
Pomwepo anathamanga nadza kwa Simoni Petro ndi kwa wophunzira wina amene Yesu anamkonda, nanena nao, Anacotsa Ambuye kumanda, ndipo sitidziwa kumene anamuika iye.
3
Anaturuka tsono Petro ndi wophunzira winayo, nalinkupita kumanda.
4
Koma anathamanga onse awiri pamodzi; ndipo wophunzira winayo anathamanga naposa Petro, nayamba kufika kumanda;
5
ndipo m'mene anawerama cosuzumira anaona nsaru zabafuta zitakhala, komatu sanalowamo.
6
Pamenepo anadzanso Simoni Petro alikumtsata iye, nalowa m'manda; ndipo anaona nsaru zabafuta zitakhala,
7
ndi mlezo, umene unali pamutu pace, wosakhala pamodzi ndi nsaru zabafuta, koma wopindika padera pamalo pena.
8
Pamenepo tsono analowanso wophunzira winayo, amene anayamba kufika kumanda, ndipo anaona, nakhulupira.
9
Pakuti kufikira pomwepo sanadziwa lembo lakuti ayenera iye kuuka kwa akufa.
10
Cifukwa cace akuphunzirawo anacokanso, kunka kwao.
11
Koma Mariya analikuima kumanda kunja, alikulira. Ndipo m'mene alikulira anawerama cisuzumirire kumanda;
12
ndipo anaona angelo awiri atabvala zoyera, alikukhala mmodzi kumutu, ndi wina kumiyendo, kumene mtembo wa Yesu udagona.
13
Ndipo iwowa ananena kwa iye, Mkazi, uliranji? Ananena nao, Cifukwa anacotsa Ambuye wanga, ndipo sindidziwa kumene anamuika iye.
14
M'mene adanena izi, anaceuka m'mbuy'o, naona Yesu ali ciriri, ndipo sanadziwa kuti ndiye Yesu.
15
Yesu ananena naye, Mkazi, uliranji? ufuna yani? Iyeyu poyesa kuti ndiye wakumunda, ananena ndi iye, Mbuye ngati mwamnyamula iye, ndiuzeni kumene mwamuika iye, ndipo ndidzamcotsa.
16
Yesu ananena naye, Mariya. Iyeyu m'mene anaceuka, ananena ndi iye m'Cihebri, Raboni; cimene cinenedwa, Mphunzitsi.
17
Yesu ananena naye, Usandikhudze, pakuti sindinatha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Atate wanu, ndi Mulungu wanga, ndi Mulungu wanu.
18
Mariya wa Magadala anapita nalalikira kwa akuphunzirawo, kuti, Ndaona Ambuye; ndi kuti ananena izi kwa iye.
19
Pamenepo, pokhala madzulo, tsiku lomwelo, loyamba la Sabata, makomo ali citsekere, kumene anakhala akuphunzira, cifukwa ca kuopa Ayuda, Yesu anadza naimirira pakati pao, nanena nao, Mtendere ukhale ndi inu.
20
Ndipo pamene adanena ici, anaonetsa iwo manja ace ndi nthiti zace. Pamenepo akuphunzira anakondwera pakuona Ambuye.
21
Cifukwa cace Yesu anatinso kwa iwo, Mtendere ukhale ndi inu; monga Atate wandituma Ine, Inenso ndituma inu.
22
Ndipo pamene anati ici anawapumira, nanena nao, Landirani Mzimu Woyera.
23
Zocimwa za anthu ali onse muwakhululukira, zikhululukidwa kwa iwo; za iwo amene muzigwiritsa, zagwiritsidwa.
24
Koma Tomasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, wochedwa Didimo, sanakhala nao pamodzi, pamene Yesu anadza.
25
Cifukwa cace akuphunzira ena ananena naye, Tamuona Ambuye. Koma iye anati kwa iwo, Ndikapanda kuona m'manja ace cizindikilo ca misomaliyo, ndi kuika cala canga m'cizindikilo ca misomaliyo, ndi kuika dzanja langa ku nthiti yace; sindidzakhulupira.
26
Ndipo pakupita masiku asanu ndi atatu akuphunzira ace analinso m'nyumbamo, ndi Tomasi pamodzi nao: Yesu anadza, makomo ali citsekere, naimirira pakati, nati, Mtendere ukhale ndi inu.
27
Pomwepo ananena kwa Tomasi, Bwera naco cala cako kuno, nuone manja anga; ndipo bwera nalo dzanja lako, nuliike ku nthiti yanga, ndipo usakhale wosakhulupira, koma wokhulupira.
28
Tomasi anayankha nati kwa iye, Ambuye wanga, ndi Mulungu wanga.
29
Yesu ananena kwa iye, Cifukwa wandiona Ine, wakhulupira; odala iwo akukhulupira, angakhale sanaona.
30
Ndipo zizindikilo zina zambiri Yesu anazicita pamaso pa akuphunzira ace, zimene sizinalembedwa m'buku ili;
31
koma zalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Kristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupira mukhale nao moyo m'dzina lace.
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21