bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Malachi 4
Malachi 4
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
1
Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akucita coipa, adzakhala ngati ciputu; ndi tsiku lirinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.
2
Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la cilungamo lidzakuturukirani, muli kuciritsa m'mapiko mwace; ndipo mudzaturuka ndi kutumphatumpha ngati ana a ng'ombe onenepa,
3
Ndipo mudzapondereza oipa; pakuti adzakhala ngati mapulusa ku mapazi anu, tsiku ndidzaikalo, ati Yehova wamakamu.
4
Kumbukilani cilamulo ca Mose mtumiki wanga, ndinamlamuliraco m'Horebu cikhale ca Israyeli lonse, ndico malemba ndi maweruzo.
5
Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikuru ndi loopsa la Yehova.
6
Ndipo adzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate ao; kuti ndisafike ndi kukantha dziko lionongeke konse.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
All chapters:
1
2
3
4