bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Mark 16
Mark 16
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
1
Ndipo litapita Sabata, Maliya wa Magadala, ndi Maliya amace wa Yakobo, ndi Salome, anagula zonunkhira, kuti akadze kumdzoza Iye.
2
Ndipo anadza kumanda mamawa tsiku loyamba la Sabata, litaturuka dzuwa.
3
Ndipo analikunena mwa okha, Adzatikunkhunizira ndam mwalawo, pa khomo la manda?
4
Ndipo pamene anakweza maso anaona kuti mwala wakunkhunizidwa pakuti unali waukuru ndithu.
5
Ndipo pamene analowa m'manda, anaona mnyamata alikukhala ku mba li va ku dzanja lamanja, wobvala mwinjiro woyera; ndipo iwo anadabwa.
6
Ndipo iye ananena nao, Musadabwe: mulikufuna Yesu Mnazarene amene anapacikidwa: anauka; sali pano; taonani, mbuto m'men e anaikamo Iye!
7
Koma mukani, uzani ophunzira ace, ndi Petro, kuti akutsogolerani inu ku Galileya; kumeneko mudzamuona Iye, monga ananena ndi inu.
8
Ndipo anaturuka iwo, nathawa kumanda; pakuti kunthunthumira ndi kudabwa kwakukuru kudawagwira; ndipo sanauza kanthu kwa munthu ali yense; pakuti anacitamantha.
9
Ndipo pamene Iye adauka mamawa tsiku loyamba la sabata, anayamba kuonekera kwa Maliya wa Magadala, amene Iye adamturutsira ziwanda zisanu ndi ziwiri.
10
Iyeyu anapita kuwauza iwo amene adafokhala naye, ali ndi cisoni ndi kulira misozi.
11
Ndipo iwowo, pamene anamva kuti ali moyo, ndi kuti adapenyeka kwa iye, sanamvera.
12
Ndipo zitatha izi, anaonekanso Iye m'maonekedwe ena kwa awiri a iwo alikuyenda kupita kumiraga,
13
Ndipo iwowa anacoka nawauza otsala; koma iwo omwe sanawabvomereza.
14
Ndipo citatha ico anaonekera kwa khumi ndi mmodzi iwo okha, alikuseama pacakudya; ndipo anawadzudzula cifukwa ca kusabvomereza kwao ndi kuuma mtima, popeza sanabvomereza iwo amene adamuona, atauka Iye.
15
Ndipo ananena nao, mukani ku dziko lonse lapansi, lalikirani Uthenga Wabwino kwa olengedwa onse.
16
Amene akhulupirira nabatizidwa, adzapulumutsidwa; koma amene sakhulupirira adzalangidwa.
17
Ndipo zizindikilo izi zidzawatsata iwo akukhulupirira; m'dzina langa adzaturutsa ziwanda; adzalankhula ndi malankhulidwe atsopano;
18
adzatola njoka, ndipo ngakhale akamwa kanthu kakufa nako, sikadzawapweteka; adzaika manja ao pa odwala, ndipo adzacira.
19
Pamenepo Ambuye Yesu, ata-tha kulankhula nao, analandiridwa Kumwamba, nakhala pa dzanja lamanja la Mulungu.
20
Ndipo iwowa anaturuka, nalalikira ponse ponse, ndipo Ambuye anacita nao pamodzi, natsimikiza mau ndi zizindikilo zakutsatapo, Amen.
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16