bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Matthew 7
Matthew 7
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 8 →
1
Musaweruze, kuti mungaweruzidwe.
2
Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso.
3
Ndipo upenya bwanji kacitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda uli m'diso la iwe mwini suuganizira?
4
Kapena udzati bwanji kwa mbale wako, Tandilola ndicotse kacitsotso m'diso lako; ndipo ona, mtandawo ulimo m'diso lakoli.
5
Wonyenga iwe! tayamba kucotsa m'diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kucotsa kacitsotso m'diso la mbale wako.
6
Musamapatsa copatulikaco kwa agaru, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.
7
Pemphani, ndipo cidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo cidzatsegulidwa kwa inu;
8
pakuti yense wakupempha alandira; ndi wakufunayo apeza; ndi kwa wogogodayo citsegulldwa.
9
Kapena munthu ndani wa inu, amene pompempha mwana wace mkate, adzampatsa mwala?
10
Kapena pompempha nsomba, adzampatsa iye njoka kodi?
11
Comweco, ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye?
12
Cifukwa cace zinthu ziri zonse mukafuna kuti anthu acitire inu, inunso muwacitire iwo zotero; pakuti ico ndico cilamulo ndi aneneri.
13
Lowani pa cipata copapatiza; cifukwa cipata ciri cacikuru, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka iri yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa ico.
14
Pakuti cipata ciri copapatiza, ndi icepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akucipeza cimeneco ali owerengeka.
15
Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zobvala zankhosa, koma m'kati mwao ali afisi alusa.
16
Mudzawazindikira ndi zipatso zao. Kodi achera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula?
17
Comweco mtengo wabwino uli wonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuci upatsa zipatso zoipa,
18
Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuci kupatsa zipatso zokoma.
19
Mtengo uli wonse wosapatsa cipatso cokoma, audula, nautaya kumoto.
20
Inde comweco pa zipatso zao mudzawazindikira iwo.
21
Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakucitayo cifuniro ca Atate wanga wa Kumwamba.
22
Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mau m'dzina lanu, ndi m'dzina lanunso kuturutsa mizimu yoipa, ndi kucita m'dzina lanunso zamphamvu zambiri?
23
Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziwani inu nthawi zonse; cokani kwa Ine, inu akucita kusayeruzika.
24
Cifukwa cimeneci yense amene akamva mau anga amenewa, ndi kuwacita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wocenjera, amene anamanga nyumba yace pathanthwe;
25
ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; koma siinagwa; cifukwa inakhazikika pathanthwepo.
26
Ndipo yense akamva mau anga amenewa, ndi kusawacita, adzafanizidwa ndi munthu wopusa, yemwe anamanga nyumba yace pamcenga;
27
ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwace kunali kwakukuru.
28
Ndipo panakhala pamene Yesu anatha mau amenewa, makamu a anthu anazizwa ndi ciphunzitso cace:
29
pakuti anawaphunzitsa monga mwini mphamvu, wosanga alembiao.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28