bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
1 Corinthians 10
1 Corinthians 10
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 11 →
1
Pakuti sindifuna, kuti mukhale osadziwa, abale, kuti makolo athu onse anali pansi pa mtambo, naoloka nyanja onse;
2
nabatizidwa onse kwa Mose, mumtambo, ndi m'nyanja,
3
nadya onse chakudya chauzimu chimodzimodzi;
4
namwa onse chakumwa chauzimu chimodzimodzi; pakuti anamwa mwa thanthwe lauzimu lakuwatsata; koma thanthwelo ndiye Khristu.
5
Koma ochuluka a iwo Mulungu sanakondwera nao; pakuti anamwazika m'chipululu.
6
Koma zinthu izi zinachitika, zikhale zotichenjeza ife, kuti tisalakalake zoipa ife, monganso iwowo analakalaka.
7
Kapena musakhale opembedza mafano, monga ena a iwo, monga kwalembedwa, Anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nanyamuka kusewera.
8
Kapena tisachite dama monga ena a iwo anachita dama, nagwa tsiku limodzi zikwi makumi awiri ndi zitatu.
9
Kapena tisayese Ambuye, monga ena a iwo anayesa, naonongeka ndi njoka zija.
10
Kapena musadandaula, monga ena a iwo anadandaula, naonongeka ndi woonongayo.
11
Koma izi zinachitika kwa iwowa monga zotichenjeza, ndipo zinalembedwa kutichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthawi ya pansi pano adafika pa ife.
12
Chifukwa chake iye wakuyesa kuti ali chilili, ayang'anire kuti angagwe.
13
Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.
14
Chifukwa chake, okondedwa anga, thawani kupembedza mafano.
15
Ndinena monga kwa anzeru; lingirirani inu chimene ndinena.
16
Chikho cha dalitso chimene tidalitsa, sichili chiyanjano cha mwazi wa Khristu kodi? Mkate umene tinyema suli chiyanjano cha thupi la Khristu kodi?
17
Pakuti mkate ndiwo umodzi, chotero ife ambiri ndife thupi limodzi; pakuti ife tonse titengako kumkate umodzi.
18
Tapenyani Israele monga mwa thupi; kodi iwo akudya nsembezo alibe chiyanjano ndi guwa la nsembe?
19
Ndinena chiyani tsono? Kuti choperekedwa nsembe kwa mafano chili kanthu? Kapena kuti fano lili kanthu kodi?
20
Koma nditi kuti zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziwanda osati kwa Mulungu; ndipo sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziwanda.
21
Simungathe kumwera chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziwanda; simungathe kulandirako kugome la Ambuye, ndi kugome la ziwanda.
22
Kapena kodi tichititsa nsanje Ambuye? Kodi mphamvu zathu ziposa Iye?
23
Zinthu zonse ziloleka; koma sizipindula zonse. Zinthu zonse ziloleka; koma sizimanga zonse.
24
Munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake.
25
Chonse chogulitsidwa pa msika wa nyama, mudye, osafunsa kanthu chifukwa cha chikumbu mtima;
26
pakuti dziko lapansi lili la Ambuye, ndi kudzala kwake.
27
Ngati wina wa osakhulupirira akuitanani, ndipo mufuna kupita; mudye chomwe chiikidwa kwa inu, osafunsa kanthu, chifukwa cha chikumbu mtima.
28
Koma ngati wina akati kwa inu, Yoperekedwa nsembe iyi, musadye, chifukwa cha iyeyo wakuuza, ndi chifukwa cha chikumbu mtima.
29
Ndinena chikumbu mtima, si cha iwe mwini, koma cha winayo; pakuti ufulu wanga uyesedwa ninji ndi chikumbu mtima cha wina?
30
Ngati ine ndilandirako mwachisomo, ndinenezedwa bwanji chifukwa cha ichi chimene ndiyamikapo?
31
Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.
32
Khalani osakhumudwitsa, kapena Ayuda, kapena Agriki, kapena Mpingo wa Mulungu;
33
monga inenso ndikondweretsa onse m'zinthu zonse, wosafuna chipindulo changa, koma cha unyunjiwo, kuti apulumutsidwe.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16