bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
1 Thessalonians 3
1 Thessalonians 3
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 4 →
1
Chifukwa chake, posakhoza kulekereranso, tidavomereza mtima atisiye tokha ku Atene;
2
ndipo tinatuma Timoteo, mbale wathuyo ndi mtumiki wa Mulungu m'Uthenga Wabwino wa Khristu, kuti akhazikitse inu, ndi kutonthoza inu za chikhulupiriro chanu;
3
kuti asasunthike wina ndi zisautso izi, pakuti mudziwa nokha kuti adatiika ife tichite izi.
4
Pakutinso, pamene tinali ndi inu tinakuuziranitu kuti tidzamva zisautso; monga kudachitika, monganso mudziwa.
5
Mwa ichi inenso, posalekereranso, ndinatuma kukazindikira chikhulupiriro chanu, kuti kapena woyesa akadakuyesani, ndipo chivuto chathu chikadakhala chopanda pake.
6
Koma tsopano pofika Timoteo kwathu kuchokera kwa inu, ndi kutifotokozera mbiri yokoma ya chikhulupiriro ndi chikondano chanu, ndi kuti mutikumbukira bwino masiku onse, pokhumba kutiona ife, monganso ife kukuonani inu;
7
chifukwa cha ichi tasangalala pa inu, abale, m'kupsinjika kwathu konse ndi chisautso chathu chonse, mwa chikhulupiriro chanu;
8
pakuti tsopano tili ndi moyo, ngati inu muchilimika mwa Ambuye.
9
Pakuti tikhoza kubwezera kwa Mulungu chiyamiko chanji chifukwa cha inu, pa chimwemwe chonse tikondwera nacho mwa inu pamaso pa Mulungu wathu;
10
ndi kuchulukitsa mapemphero athu usiku ndi usana kuti tikaone nkhope yanu, ndi kukwaniritsa zoperewera pa chikhulupiriro chanu?
11
Koma Mulungu Atate wathu mwini yekha, ndi Ambuye wathu Yesu atitsogolere m'njira yakufika kwa inu;
12
koma Ambuye akukulitseni inu, nakuchulukitseni m'chikondano wina kwa mnzake ndi kwa anthu onse, monganso ife titero kwa inu;
13
kuti akakhazikitse mitima yanu yopanda chifukwa m'chiyero pamaso pa Mulungu Atate wathu, pakufika Ambuye wathu Yesu pamodzi ndi oyera mtima ake onse.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5