bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
1 Timothy 5
1 Timothy 5
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 6 →
1
Mkulu usamdzudzule, komatu umdandaulire ngati atate; anyamata ngati abale;
2
akazi akulu ngati amai; akazi aang'ono ngati alongo, m'kuyera mtima konse.
3
Chitira ulemu amasiye amene ali amasiye ndithu.
4
Koma ngati wamasiye wina ali nao ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m'banja lao, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.
5
Koma iye amene ali wamasiye ndithu, nasiyidwa yekha, ayembekezera Mulungu, nakhalabe m'mapembedzo ndi mapemphero usiku ndi usana.
6
Koma iye wakutsata zomkondweretsa, adafa pokhala ali ndi moyo.
7
Ndipo izi ulamulire, kuti akhale opanda chilema.
8
Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.
9
Asawerengedwe wamasiye ngati sanafikire zaka makumi asanu ndi limodzi, atakhala mkazi wa mwamuna mmodzi,
10
wa mbiri ya ntchito zabwino; ngati walera ana, ngati wachereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a oyera mtima, ngati wathandiza osautsidwa, ngati anatsatadi ntchito zonse zabwino.
11
Koma amasiye ang'ono uwakane; pakuti pamene ayamba kumchitira Khristu chipongwe afuna kukwatiwa;
12
pokhala nacho chitsutso, popeza adataya chikhulupiriro chao choyamba.
13
Ndipo aphunziraponso kuchita ulesi, aderuderu; koma osati ulesi wokha, komatunso alankhula zopanda pake, nachita mwina ndi mwina, olankhula zosayenera.
14
Chifukwa chake nditi akwatiwe amasiye ang'ono, nabale ana, naweruzire nyumba, osapatsa chifukwa kwa mdaniyo chakulalatira;
15
pakuti adayamba ena kupatuka ndi kutsata Satana.
16
Ngati mkazi wina wokhulupirira ali nao amasiye, iye awathandize, ndipo Mpingowo usalemedwe; kuti uthandize iwo amene ali amasiye ndithu.
17
Akulu akuweruza bwino ayesedwe oyenera ulemu wowirikiza, makamaka iwo akuchititsa m'mau ndi m'chiphunzitso.
18
Pakuti malembo ati, Usapunamiza ng'ombe yopuntha tirigu. Ndipo Wogwira ntchito ayenera kulipira kwake.
19
Pa mkulu usalandire chomnenera, koma pakhale mboni ziwiri kapena zitatu.
20
Iwo akuchimwa uwadzudzule pamaso pa onse, kuti otsalawo achite mantha.
21
Ndikuchitira umboni pamaso pa Mulungu, ndi Khristu Yesu, ndi angelo osankhika, kuti usunge izi kopanda kusankhiratu, wosachita kanthu monga mwa tsankho.
22
Usafulumira kuika manja pa munthu aliyense, kapena usayanjana nazo zoipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima.
23
Usakhalenso wakumwa madzi okha, komatu uchite naye vinyo pang'ono, chifukwa cha mimba yako ndi zofooka zako zobwera kawirikawiri.
24
Zochimwa za anthu ena zili zooneka kale, zitsogola kunka kumlandu; koma enanso ziwatsata.
25
Momwemonso pali ntchito zokoma zinaonekera kale; ndipo zina zosati zotere sizikhoza kubisika.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6