bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
2 Timothy 3
2 Timothy 3
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 4 →
1
Koma zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthawi zowawitsa.
2
Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika,
3
osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudierekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino,
4
achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu;
5
akukhala nao maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.
6
Pakuti mwa iwo akhala akukwawira m'nyumba, nagwira akazi opusa, osenza akatundu a zoipa zao, otengedwa nazo zilakolako za mitundumitundu:
7
ophunzira nthawi zonse, koma sakhoza konse kufikira kuchizindikiritso cha choonadi.
8
Ndipo monga momwe Yane ndi Yambere anatsutsana naye Mose, kotero iwonso atsutsana nacho choonadi; ndiwo anthu ovunditsitsa mtima, osatsimikizidwa pachikhulupiriro.
9
Koma sadzapitirirapo; pakuti kupusa kwao kudzaonekeratu kwa onse, monganso kupusa kwa iwo aja.
10
Koma iwe watsatatsata chiphunzitso changa, mayendedwe, chitsimikizo mtima, chikhulupiriro, kuleza mtima, chikondi, chipiriro,
11
mazunzo, kumva zowawa; zotere zonga anandichitira m'Antiokeya, m'Ikonio, m'Listara, mazunzo otere onga ndawamva; ndipo m'zonsezi Ambuye anandilanditsa.
12
Ndipo onse akufuna kukhala opembedza m'moyo mwa Khristu Yesu, adzamva mazunzo.
13
Koma anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.
14
Koma ukhalebe iwe mu izi zimene waziphunzira, nutsimikizika mtima nazo, podziwa amene adakuphunzitsa;
15
ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.
16
Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m'chilungamo:
17
kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4