bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Exodus 1
Exodus 1
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 2 →
1
Ndipo maina a ana a Israele, amene analowa m'Ejipito ndi Yakobo ndi awa, analowa munthu ndi banja lake:
2
Rubeni, Simeoni, Levi ndi Yuda;
3
Isakara, Zebuloni, ndi Benjamini;
4
Dani ndi Nafutali, Gadi ndi Asere.
5
Ndipo amoyo onse amene anatuluka m'chuuno mwake mwa Yakobo ndiwo makumi asanu ndi awiri; koma Yosefe anali m'Ejipito.
6
Ndipo anafa Yosefe, ndi abale ake onse, ndi mbadwo uwo wonse.
7
Ana a Israele ndipo anaswana, nabalana, nachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu; ndipo dziko linadzala nao.
8
Pamenepo inalowa mfumu yatsopano m'ufumu wa Ejipito, imene siinadziwa Yosefe.
9
Ndipo ananena ndi anthu ake, Taonani, anthu, ndiwo ana a Israele, achuluka, natiposa mphamvu.
10
Tiyeni, tiwachenjerere angachuluke, ndi kuphatikizana ndi adani athu ikafika nkhondo, ndi kulimbana nafe, ndi kuchoka m'dzikomo.
11
Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu ao. Ndipo anammangira Farao midzi yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramsesi.
12
Koma monga momwe anawasautsiramo, momwemo anachuluka, momwemonso anafalikira. Ndipo anavutika chifukwa cha ana Israele.
13
Ndipo Aejipito anawagwiritsa ana a Israele ntchito yosautsa;
14
nawawitsa moyo wao ndi ntchito yolimba, ya dothi ndi ya njerwa, ndi ntchito zonse za pabwalo, ntchito zao zonse zimene anawagwiritsa nzosautsa.
15
Ndipo mfumu ya Aejipito inanena ndi anamwino a Ahebri, dzina lake la wina ndiye Sifira, dzina la mnzake ndiye Puwa;
16
ninati, Pamene muchiza akazi a Ahebri nimuwaone pamipando; akakhala mwana wamwamuna, mumuphe; akakhala wamkazi, akhale ndi moyo.
17
Koma anamwino anaopa Mulungu, ndipo sanachite monga mfumu ya Aejipito inawauza, koma analeka ana amuna akhale ndi moyo.
18
Ndipo mfumu ya Aejipito inaitana anamwino, ninena nao, Mwachita ichi chifukwa ninji, ndi kuleka ana amunawo akhale ndi moyo?
19
Ndipo anamwino ananena ndi Farao, Popeza akazi a Ahebri safanana ndi akazi a Aejipito; pakuti ali ndi mphamvu, naona ana asanafike anamwino.
20
Potero Mulungu anawachitira zabwino anamwino; ndipo anthuwo anachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu.
21
Ndipo kunatero kuti, popeza anamwino anaopa Mulungu, Iye anawamangitsira mabanja.
22
Ndipo Farao analamulira anthu ake onse, ndi kuti, Ana amuna onse akabadwa aponyeni m'nyanja, koma ana akazi onse alekeni amoyo.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40