bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Habakkuk 1
Habakkuk 1
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 2 →
1
Katundu adamuona mneneri Habakuku
2
Yehova, ndidzafuula mpaka liti osamva Inu? Ndifuulira kwa Inu za chiwawa, koma simupulumutsa.
3
Mundionetseranji zopanda pake, ndi kundionetsa zovuta? Pakuti kufunkha ndi chiwawa zili pamaso panga; ndipo pali ndeu, nauka makani.
4
Pakuti chilamulo chalekeka, ndi chiweruzo sichitulukira konse; popeza woipa azinga wolungama, chifukwa chake chiweruzo chituluka chopindika.
5
Penyani mwa amitundu, penyetsetsani, nimudabwe kwakukulu, pakuti ndichita ntchito masiku anu, imene simudzavomera chinkana akufotokozerani.
6
Pakuti taonani, ndiukitsa Ababiloni, mtundu uja wowawa ndi waliwiro, wopitira pa chitando cha dziko lapansi, kulowa m'malo mosati mwao, mukhale mwaomwao.
7
Ali oopsa, achititsa mantha, chiweruzo chao ndi ukulu wao zituluka kwa iwo eni.
8
Akavalo ao aposa anyalugwe liwiro lao, aposa mimbulu ya madzulo ukali wao, ndipo apakavalo ao atanda; inde apakavalo ao afumira kutali; auluka ngati chiombankhanga chofulumira kudya.
9
Adzera chiwawa onsewo; nkhope zao zikhazikika zolunjika m'tsogolo; asonkhanitsa andende ngati mchenga.
10
Inde anyoza mafumu, aseka akalonga; aseka linga lililonse; popeza aunjika dothi, nalilanda.
11
Pamenepo adzapitirira ngati mphepo, nadzalakwa ndi kupalamula, iye amene aiyesa mphamvu yake mulungu wake.
12
Si ndinu wachikhalire, Yehova Mulungu wanga, wopatulika wanga? Sitidzafa. Yehova munamuikiratu kuti aweruzidwe; ndipo Inu, Thanthwe, munamkhazika kuti alangidwe.
13
Inu wa maso osalakwa, osapenya choipa, osakhoza kupenyerera chovuta, mupenyereranji iwo akuchita mochenjerera, ndi kukhala chete pamene woipa ammeza munthu wolungama woposa iye mwini;
14
ndi kuyesa anthu ngati nsomba za m'nyanja, ngati zokwawa zopanda wakuzilamulira.
15
Aziwedza zonse ndi mbedza, azigwira m'ukonde wake, nazisonkhanitsa m'khoka mwake; chifukwa chake asekera nakondwerera.
16
Chifukwa chake aphera nsembe ukonde wake, nafukizira khoka lake, pakuti mwa izi gawo lake lilemera, ndi chakudya chake chichuluka.
17
Kodi m'mwemo adzakhuthula m'ukonde mwake osaleka kuphabe amitundu?
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3