bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Hebrews 3
Hebrews 3
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 4 →
1
Potero, abale oyera mtima, olandirana nao maitanidwe akumwamba, lingirirani za Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chivomerezo chathu, Yesu;
2
amene anakhala wokhulupirika kwa Iye adamuikayo, monganso Mose m'nyumba yake yonse.
3
Pakuti ameneyo wayesedwa woyenera ulemerero woposa Mose, monga momwe iye amene anaimanga nyumba ali nao ulemerero woposa nyumbayi.
4
Pakuti nyumba iliyonse ili naye wina woimanga; koma wozimanga zonse ndiye Mulungu.
5
Ndipo Mosetu anali wokhulupirika m'nyumba yake yonse, monga mnyamata, achitire umboni izi zidzalankhulidwazi;
6
koma Khristu monga mwana, wosunga nyumba yake; ndife nyumba yake, ngati tigwiritsa kulimbika mtima ndi kudzitamandira kwa chiyembekezocho, kuchigwira kufikira chitsiriziro.
7
Momwemo, monga anena Mzimu Woyera, Lero ngati mudzamva mau ake,
8
musaumitse mitima yanu, monga m'kupsetsa mtimamo, monga muja tsiku la chiyesero m'chipululu,
9
chimene makolo anu anandiyesa nacho, ndi kundivomereza, naona ntchito zanga zaka makumi anai.
10
Momwemo ndinakwiya nao mbadwo uwu, ndipo ndinati, Nthawi zonse amasochera mumtima; koma sanazindikira njira zanga iwowa;
11
Monga ndinalumbira m'ukali wanga: Ngati adzalowa mpumulo wanga!
12
Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;
13
komatu dandaulirananani nokha tsiku ndi tsiku, pamene patchedwa, Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjerero la uchimo;
14
pakuti takhala ife olandirana ndi Khristu, ngatitu tigwiritsa chiyambi cha kutama kwathu kuchigwira kufikira chitsiriziro;
15
umo anenamo, Lero ngati mudzamva mau ake, musaumitse mitima yanu, monga pa kupsetsa mtima.
16
Pakuti ndi ayani, pakumva, anapsetsa mtima? Kodi si onse aja adatuluka m'Ejipito ndi Mose?
17
Koma anakwiya ndi ayani zaka makumi anai? Kodi si ndi awo adachimwawo, amene matupi ao adagwa m'chipululu?
18
Ndipo adawalumbirira ayani kuti asalowe mpumulo wake?
19
Si awo kodi osamverawo? Ndipo tiona kuti sanakhoza kulowa chifukwa cha kusakhulupirira.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13