bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
John 1
John 1
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 2 →
1
Pachiyambi panali Mau, ndipo Mau anali kwa Mulungu, ndipo Mau ndiye Mulungu.
2
Awa anali pachiyambi kwa Mulungu.
3
Zonse zinalengedwa ndi Iye; ndipo kopanda Iye sikunalengedwa kanthu kalikonse kolengedwa.
4
Mwa Iye munali moyo; ndi moyowu unali kuunika kwa anthu.
5
Ndipo kuunikaku kunawala mumdima; ndi mdimawu sunakuzindikira.
6
Kunali munthu, wotumidwa ndi Mulungu, dzina lake ndiye Yohane.
7
Iyeyu anadza mwa umboni kudzachita umboni za kuunikaku, kuti onse akakhulupirire mwa iye.
8
Iye sindiye kuunikaku, koma anatumidwa kukachita umboni wa kuunikaku.
9
Uku ndiko kuunika kwenikweni, kumene kuunikira anthu onse akulowa m'dziko lapansi.
10
Anali m'dziko lapansi, ndi dziko linalengedwa ndi Iye, koma dziko silinamzindikira Iye.
11
Anadza kwa zake za Iye yekha, ndipo ake a mwini yekha sanamlandire Iye.
12
Koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake;
13
amene sanabadwe ndi mwazi, kapena ndi chifuniro cha thupi, kapena ndi chifuniro cha munthu, koma cha Mulungu.
14
Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.
15
Yohane achita umboni za Iye, nafuula nati, Uyu ndiye amene ndinanena za Iye, Wakudzayo pambuyo panga analipo ndisanabadwe ine; chifukwa anakhala woyamba wa ine.
16
Chifukwa mwa kudzala kwake tinalandira ife tonse, chisomo chosinthana ndi chisomo.
17
Chifukwa chilamulo chinapatsidwa mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinadza mwa Yesu Khristu.
18
Kulibe munthu anaona Mulungu nthawi zonse; Mwana wobadwa yekha wakukhala pa chifuwa cha Atate, Iyeyu anafotokozera.
19
Ndipo umene ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayuda anatuma kwa iye ansembe ndi Alevi a ku Yerusalemu akamfunse iye, Ndiwe yani?
20
Ndipo anavomera, wosakana; nalola kuti, Sindine Khristu.
21
Ndipo anamfunsa iye, Nanga bwanji? Ndiwe Eliya kodi? Nanena iye, Sindine iye. Ndiwe Mneneriyo kodi? Nayankha, Iai.
22
Chifukwa chake anati kwa iye, Ndiwe yani? Kuti tibwezere mau kwa iwo anatituma ife. Unena chiyani za iwe wekha?
23
Anati, Ndine mau a wofuula m'chipululu, Lungamitsani njira ya Mbuye, monga anati Yesaya mneneriyo.
24
Ndipo otumidwawo anali a kwa Afarisi.
25
Ndipo anamfunsa iye, nati kwa iye, Koma ubatiza bwanji, ngati suli Khristu, kapena Eliya, kapena Mneneriyo?
26
Yohane anawayankha, nati, Ine ndibatiza ndi madzi; pakati pa inu paimirira amene simumdziwa,
27
ndiye wakudza pambuyo panga, amene sindiyenera kummasulira lamba la nsapato yake.
28
Zinthu izi zinachitika m'Betaniya tsidya lija la Yordani, pomwe analikubatiza Yohane.
29
M'mawa mwake anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!
30
Ndiye amene ndinati za Iye, Pambuyo panga palinkudza munthu amene analipo ndisanabadwe ine; pakuti anali woyamba wa ine.
31
Ndipo sindinamdziwa Iye; koma kuti aonetsedwe kwa Israele, chifukwa cha ichi ndinadza ine kudzabatiza ndi madzi.
32
Ndipo Yohane anachita umboni, nati, Ndinaona Mzimu alikutsika kuchokera Kumwamba monga nkhunda; nakhalabe pa Iye.
33
Ndipo sindinamdziwa Iye, koma wonditumayo kudzabatiza ndi madzi, Iyeyu ananena ndi ine, Amene udzaona Mzimu atsikira, nakhala pa Iye, yemweyu ndiye wakubatiza ndi Mzimu Woyera.
34
Ndipo ndaona ine, ndipo ndachita umboni kuti Mwana wa Mulungu ndi Yemweyu.
35
M'mawa mwakenso analikuimirira Yohane ndi awiri a ophunzira ake;
36
ndipo poyang'ana Yesu alikuyenda, anati, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu!
37
Ndipo ophunzira awiriwo anamva iye alinkulankhula, natsata Yesu.
38
Koma Yesu anacheuka, napenya iwo alikumtsata, nanena nao, Mufuna chiyani? Ndipo anati kwa Iye, Rabi (ndiko kunena posandulika, Mphunzitsi), mukhala kuti?
39
Nanena nao, Tiyeni, mukaone. Pamenepo anadza naona kumene anakhala; nakhala ndi Iye tsiku lomwelo; panali monga ora lakhumi.
40
Andrea mbale wake wa Simoni Petro anali mmodzi wa awiriwo, anamva Yohane, namtsata Iye.
41
Anayamba iye kupeza mbale wake yekha Simoni, nanena naye, Tapeza ife Mesiya (ndiko kusandulika Khristu).
42
Anadza naye kwa Yesu. M'mene anamyang'ana iye, anati, Uli Simoni mwana wa Yohane; udzatchedwa Kefa (ndiko kusandulika Petro).
43
M'mawa mwake anafuna kutuluka kunka ku Galileya, napeza Filipo. Ndipo Yesu ananena naye, Tsata Ine.
44
Koma Filipo anali wa ku Betsaida, mudzi wa Andrea ndi Petro.
45
Filipo anapeza Natanaele, nanena naye, Iye amene Mose analembera za Iye m'chilamulo, ndi aneneri, tampeza, ndiye Yesu mwana wa Yosefe wa ku Nazarete.
46
Natanaele anati kwa iye, Ku Nazarete nkutha kuchokera kanthu kabwino kodi? Filipo ananena naye, Tiye ukaone.
47
Yesu anaona Natanaele alinkudza kwa Iye, nanena za iye, Onani, Mwisraele ndithu, mwa iye mulibe chinyengo!
48
Natanaele ananena naye, Munandidziwira kuti? Yesu anayankha nati kwa iye, Asanakuitane Filipo, pokhala iwe pansi pa mkuyu paja, ndinakuona iwe.
49
Natanaele anayankha Iye, Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu mfumu ya Israele.
50
Yesu anayankha nati kwa iye, Chifukwa ndinati kwa iwe kuti ndinakuona pansi pa mkuyu ukhulupirira kodi? Udzaona zoposa izi.
51
Ndipo ananena naye, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mudzaona thambo lotseguka, ndi angelo a Mulungu akwera natsikira pa Mwana wa Munthu.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21