bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Luke 17
Luke 17
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 18 →
1
Ndipo anati kwa ophunzira ake, Sikutheka kuti zolakwitsa zisadze; koma tsoka iye amene adza nazo.
2
Kukolowekedwa mwala wamphero m'khosi mwake ndi kuponyedwa iye m'nyanja nkwapafupi, koma kulakwitsa mmodzi wa ang'ono awa nkwapatali.
3
Kadzichenjerani nokha; akachimwa mbale wako umdzudzule, akalapa, umkhululukire.
4
Ndipo akakuchimwira kasanu ndi kawiri pa tsiku lake, nakakutembenukira kasanu ndi kawiri ndi kunena, Ndalapa ine; uzimkhululukira.
5
Ndipo atumwi anati kwa Ambuye, Mutionjezere chikhulupiriro.
6
Koma Ambuye anati, Mukakhala nacho chikhulupiriro ngati kambeu kampiru, mukanena kwa mtengo uwu wamkuyu, Uzulidwe, nuokedwe m'nyanja; ndipo ukadamvera inu.
7
Koma ndani mwa inu ali naye kapolo wolima, kapena woweta nkhosa, amene pobwera iye kuchokera kumunda adzanena kwa iye, Lowa tsopano, khala pansi kudya;
8
wosanena naye makamaka, Undikonzere chakudya ine, nudzimangire, nunditumikire kufikira ndadya ndi kumwa; ndipo nditatha ine udzadya nudzamwa iwe?
9
Kodi ayamika kapoloyo chifukwa anachita zolamulidwa?
10
Chotero inunso m'mene mutachita zonse anakulamulirani, nenani, Ife ndife akapolo opanda pake, tangochita zimene tayenera kuzichita.
11
Ndipo kunali, pakumuka ku Yerusalemu Iye analikupita pakati pa Samariya ndi Galileya.
12
Ndipo m'mene analowa Iye m'mudzi wina, anakomana naye amuna khumi akhate, amene anaima kutali;
13
ndipo iwo anakweza mau, nanena, Yesu, Mbuye, mutichitire chifundo.
14
Ndipo pakuwaona anati kwa iwo, Pitani, kadzionetseni nokha kwa ansembe. Ndipo kunali, m'kumuka kwao, anakonzedwa.
15
Ndipo mmodzi wa iwo, pakuona kuti anachiritsidwa, anabwerera m'mbuyo, nalemekeza Mulungu ndi mau akulu;
16
ndipo anagwa nkhope yake pansi kumapazi ake, namyamika Iye; ndipo anali Msamariya ameneyo.
17
Ndipo Yesu anayankha nati, Kodi sanakonzedwe khumi? Koma ali kuti asanu ndi anai aja?
18
Akubwera kulemekeza Mulungu sanapezeka mmodzi kodi, koma mlendo uyu?
19
Ndipo anati kwa iye, Nyamuka, nupite; chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe.
20
Ndipo pamene Afarisi anamfunsa Iye, kuti, Ufumu wa Mulungu ukudza liti, anawayankha, nati, Ufumu wa Mulungu sukudza ndi maonekedwe;
21
ndipo sadzanena, Taonani uwu, kapena uwo! Pakuti, taonani, Ufumu wa Mulungu uli m'kati mwa inu.
22
Ndipo anati kwa ophunzira ake, Adzadza masiku, amene mudzakhumba kuona limodzi la masiku a Mwana wa Munthu, koma simudzaliona.
23
Ndipo adzanena ndi inu, Taonani ilo! Taonani ili? Musachoka kapena kuwatsata;
24
pakuti monga mphezi ing'anipa kuchokera kwina pansi pa thambo, niunikira kufikira kwina pansi pa thambo, kotero adzakhala Mwana wa Munthu m'tsiku lake.
25
Koma ayenera athange wamva zowawa zambiri nakanidwe ndi mbadwo uno.
26
Ndipo monga kunakhala masiku a Nowa, momwemo kudzakhalanso masiku a Mwana wa Munthu.
27
Anadya, anamwa, anakwatira, anakwatiwa, kufikira tsiku lija Nowa analowa m'chingalawa, ndipo chinadza chigumula, nichiwaononga onsewo.
28
Monga momwenso kunakhala masiku a Loti; anadya, anamwa, anagula, anagulitsa, anabzala, anamanga nyumba;
29
koma tsiku limene Loti anatuluka m'Sodomu udavumba moto ndi sulufure zochokera kumwamba, ndipo zinawaononga onsewo;
30
momwemo kudzakhala tsiku lakuvumbuluka Mwana wa Munthu.
31
Tsikulo iye amene adzakhala pamwamba pa chindwi, ndi akatundu ake m'nyumba, asatsike kuwatenga; ndipo iye amene ali m'munda modzimodzi asabwere ku zake za m'mbuyo.
32
Kumbukirani mkazi wa Loti.
33
Iye aliyense akafuna kusunga moyo wake adzautaya, koma iye aliyense akautaya, adzausunga.
34
Ndinena ndi inu, usiku womwewo adzakhala awiri pa kama mmodzi; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa.
35
Padzakhala akazi awiri akupera pamodzi, mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa.
37
Ndipo anayankha nanena kwa Iye, Kuti, Ambuye? Ndipo anati kwa iwo, Pamene pali mtembo, pomweponso miimba idzasonkhanidwa.
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24