bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Micah 5
Micah 5
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 6 →
1
Uzisonkhana tsopano magulumagulu, mwana wamkazi wa magulu iwe; watimangira misasa, adzapanda woweruza wa Israele ndi ndodo patsaya.
2
Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza m'Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.
3
Chifukwa chake Iye adzawapereka kufikira nthawi yoti wobalayo wabala; pamenepo otsala a abale ake adzabwera pamodzi ndi ana a Israele.
4
Ndipo adzaimirira, nadzadyetsa nkhosa zake mu mphamvu ya Yehova, m'ukulu wa dzina la Yehova Mulungu wake; ndipo iwo adzakhalabe; pakuti pamenepo Iye adzakhala wamkulu kufikira malekezero a dziko lapansi.
5
Ndipo ameneyo adzakhala Mtendere; pamene a ku Asiriya adzalowa m'dziko lathu, ndi pamene adzaponda m'zinyumba zathu, tidzawaukitsira abusa asanu ndi awiri, ndi akalonga asanu ndi atatu.
6
Ndipo iwo adzatha dziko la Asiriya ndi lupanga, ndi dziko la Nimirodi, ndilo polowera pake; ndipo adzatilanditsa kwa a ku Asiriya pamene alowa m'dziko lathu, pamene aponda m'kati mwa malire athu.
7
Ndipo otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mame ochokera kwa Yehova ngati mvula paudzu, yosachedwera munthu, yosalindira ana a anthu.
8
Ndipo otsala a Yakobo adzakhala mwa amitundu, pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mkango mwa nyama zakuthengo, ngati msona wa mkango mwa magulu a nkhosa; umenewo ukapitako, upondereza, numwetula, ndipo palibe wakupulumutsa.
9
Dzanja lako likwezeke pamwamba pa iwo akuyambana nawe, ndi adani ako onse aonongeke.
10
Ndipo kudzachitika tsiku ilo, ati Yehova, ndidzaononga akavalo ako m'kati mwako, ndi kutha magaleta ako;
11
ndipo ndidzaononga midzi ya m'dziko lako, ndi kupasula malinga ako onse;
12
ndipo ndidzaononga zanyanga za m'dzanja lako; ndipo sudzakhalanso nao alosi;
13
ndidzaononganso mafano ako osema, ndi zoimiritsa zako pakati pako; ndipo sudzalambiranso ntchito za manja ako.
14
Ndipo ndidzazula zifanizo zako m'kati mwako, ndi kutha midzi yako.
15
Ndipo ndidzabwezera amitundu osamvera chilango mu mkwiyo waukali.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7