bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Nahum 2
Nahum 2
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 3 →
1
Wophwanyayo wakwera pamaso pako; sunga linga, yang'anira panjira, limbitsa m'chuuno mwako, limbikitsatu mphamvu yako.
2
Pakuti Yehova abwezeranso ukulu wake wa Yakobo ngati ukulu wake wa Israele; pakuti okhuthula anawakhuthula, naipsa nthambi zake za mpesa.
3
Zikopa za amphamvu ake zasanduka zofiira, ngwazi zivala mlangali; magaleta anyezimira ndi chitsulo tsiku la kukonzera kwake, ndi mikondo itinthidwa.
4
Magaleta achita mkokomo m'miseu, akankhana m'makwalala; maonekedwe ao akunga miuni, athamanga ngati mphezi.
5
Akumbukira omveka ake; akhumudwa m'kupita kwao, afulumira kulinga lake, ndi chotchinjiriza chakonzeka.
6
Pa zipata za mitsinje patseguka, ndi chinyumba chasungunuka.
7
Chatsimikizika, avulidwa, atengedwa, adzakazi ake alira ngati mau a nkhunda, nadziguguda pachifuwa pao.
8
Koma Ninive wakhala chiyambire chake ngati thamanda lamadzi; koma athawa. Imani, Imani! Ati, koma palibe wocheuka.
9
Funkhani siliva, funkhani golide; pakuti palibe kutha kwake kwa zosungikazo, kwa chuma cha zipangizo zofunika zilizonse.
10
Ndiye mopanda kanthu mwakemo ndi mwachabe, ndi wopasuka; ndi mtima usungunuka, ndi maondo aombana, ndi m'zuuno zonse muwawa, ndi nkhope zao zatumbuluka.
11
Ili kuti ngaka ya mikango, ndi podyera misona ya mikango, kumene mkango, waumuna ndi waukazi, ukayenda ndi mwana wa mkango, kopanda wakuiposa?
12
Mkangowo unamwetula zofikira ana ake, nusamira yaikazi yake, nudzaza mapanga ake ndi nyama, ngaka zake ndi zojiwa.
13
Taona, nditsutsana nawe, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzatentha magaleta ake m'utsi; ndi lupanga lidzadya misona yako ya mkango; ndipo ndidzachotsa zofunkha zako pa dziko lapansi, ndi mau a mithenga yako sadzamvekanso.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3