bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Nehemiah 11
Nehemiah 11
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 12 →
1
Ndipo akulu a anthu anakhala m'Yerusalemu; anthu otsala omwe anachita maere, kuti libwere limodzi la magawo khumi likhale m'Yerusalemu, mudzi wopatulika, ndi asanu ndi anai akhumi m'midzi ina.
2
Ndipo anthu anadalitsa amuna onse akudzinenera mwaufulu kuti adzakhala m'Yerusalemu.
3
Awa tsono ndi akulu a dziko okhala m'Yerusalemu; koma m'midzi ya Yuda yense anakhala pa cholowa chake m'midzi mwao, ndiwo Israele, ansembe, ndi Alevi, ndi Anetini, ndi ana a akapolo a Solomoni.
4
Ndipo m'Yerusalemu munakhala ena a ana a Yuda ndi ana a Benjamini. Mwa ana a Yuda: Ataya mwana wa Uziya, mwana wa Zekariya, mwana wa Amariya, mwana wa Sefatiya, mwana wa Mahalalele, wa ana a Perezi;
5
ndi Maaseiya mwana wa Baruki, mwana wa Kolihoze, mwana wa Hazaya, mwana wa Adaya, mwana wa Yoyaribu, mwana wa Zekariya, mwana wa Msiloni.
6
Ana onse a Perezi okhala m'Yerusalemu ndiwo ngwazi mazana anai mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi atatu.
7
Ndi ana a Benjamini ndi awa: Salu mwana wa Mesulamu, mwana wa Yoedi, mwana wa Pedaya, mwana wa Kolaya, mwana wa Maaseiya, mwana wa Itiyele, mwana wa Yesaya.
8
Ndi wotsatana naye Gabai, Salai, mazana asanu ndi anai mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.
9
Ndi Yowele mwana wa Zikiri ndiye woyang'anira wao, ndi Yuda mwana wa Hasenuwa ndiye wothandizana naye, poyang'anira mudzi.
10
Mwa ansembe: Yedaya mwana wa Yoyaribu, Yakini,
11
Seraya mwana wa Hilikiya, mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki, mwana wa Meraiyoti, mwana wa Ahitubi mtsogoleri wa m'nyumba ya Mulungu;
12
ndi abale ao ochita ntchito ya m'nyumbayi ndiwo mazana asanu ndi atatu mphambu makumi awiri kudza awiri; ndi Adaya mwana wa Yerohamu, mwana wa Pelaliya, mwana wa Amizi, mwana wa Zekariya, mwana wa Pasuri, mwana wa Malikiya;
13
ndi abale ake akulu a nyumba za makolo awiri mphambu makumi anai kudza awiri, ndi Amasisai mwana wa Azarele, mwana wa Ahazai, mwana wa Mesilemoti, mwana wa Imeri;
14
ndi abale ao, ngwazi zamphamvu, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu; ndi woyang'anira wao ndiye Zabidiele mwana wa Hagedolimu.
15
Ndi mwa Alevi: Semaya mwana wa Hasubu, mwana wa Azirikamu, mwana wa Hasabiya, mwana wa Buni;
16
ndi Sabetai, ndi Yozabadi, mwa akulu a Alevi, anayang'anira ntchito za pabwalo za nyumba ya Mulungu;
17
ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zabidi, mwana wa Asafu, ndiye mkulu wakuyamba mayamiko, popemphera; ndi Bakibukiya wotsatana naye mwa abale ake, ndi Abida mwana wa Samuwa, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni.
18
Alevi onse m'mudzi wopatulikawo ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu kudza anai.
19
Ndi odikira: Akubu, Talimoni, ndi abale ao akulindira pazipata, ndiwo zana limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri.
20
Ndi Aisraele otsala ndiwo ansembe ndi Alevi, anakhala m'midzi yonse ya Yuda, yense m'cholowa chake.
21
Koma Anetini anakhala m'Ofele, ndi Ziha, ndi Gisipa anali oyang'anira Anetini.
22
Ndipo woyang'anira wa Alevi m'Yerusalemu ndiye Uzi mwana wa Bani, mwana wa Hasabiya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mika; mwa ana a Asafu oimbira ena anayang'anira ntchito ya m'nyumba ya Mulungu.
23
Pakuti mfumu inalamulira za iwowa, naikira oimbira chowathandiza, yense chake pa tsiku lake.
24
Ndi Petahiya mwana wa Mesezabele, wa ana a Zera, mwana wa Yuda, anatumikira mfumu pa milandu yonse ya anthuwo.
25
Ndi ana ena a Yuda anakhala m'midzi ya kuminda yao, m'Kiriyati-Ariba ndi milaga yake, ndi m'Diboni ndi milaga yake, ndi m'Yekabizeele ndi midzi yake,
26
ndi m'Yesuwa, ndi m'Molada, ndi Betepeleti,
27
ndi m'Hazara-Suwala, ndi m'Beereseba ndi milaga yake,
28
ndi m'Zikilagi, ndi m'Mekona ndi milaga yake,
29
ndi m'Enirimoni, ndi m'Zora, ndi m'Yaramuti,
30
Zanowa, Adulamu ndi midzi yao, Lakisi ndi minda yake, Azeka ndi milaga yake. Ndipo anamanga misasa kuyambira ku Beereseba mpaka chigwa cha Hinomu.
31
Ana a Benjamini omwe, kuyambira ku Geba pa Mikimasi, ndi Aya, ndi pa Betele ndi milaga yake,
32
pa Anatoti, Nobi, Ananiya,
33
Hazori, Rama, Gitaimu,
34
Hadidi, Zeboimu, Nebalati,
35
Lodi, ndi Ono, chigwa cha amisiri.
36
Ndi magawo a Levi anakhala ena ku Yuda, ndi ena ku Benjamini.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13