bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Philippians 4
Philippians 4
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
1
Potero, abale anga okondedwa, olakalakidwa, ndinu chimwemwe changa ndi korona wanga, chilimikani motere mwa Ambuye, okondedwa.
2
Ndidandaulira Yuwodiya, ndidandaulira Sintike, alingirire ndi mtima umodzi mwa Ambuye.
3
Inde, ndikupemphaninso, mnzanga wa m'goli woona, muthandize akazi awa amene anakangalika nane pamodzi mu Uthenga Wabwino, pamodzi ndi Klemensinso, ndi otsala aja antchito anzanga, amene maina ao ali m'buku la Moyo.
4
Kondwerani mwa Ambuye nthawi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.
5
Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse. Ambuye ali pafupi.
6
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.
7
Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
8
Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.
9
Zimenenso mudaziphunzira, ndi kuzilandira, ndi kuzimva, ndi kuziona mwa ine, zomwezo chitani; ndipo Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi ndi inu.
10
Koma ndinakondwera mwa Ambuye kwakukulu, kuti tsopano munatsitsimukanso kulingirira mtima za kwa ine, kumenekonso munalingirirako, koma munasowa pochitapo.
11
Si kuti ndinena monga mwa chiperewero, pakuti ndaphunzira ine, kuti zindikwanire zilizonse ndili nazo.
12
Ndadziwa ngakhale kupeputsidwa, ndadziwanso kusefukira; konseko ndi m'zinthu zonse ndalowa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusowa.
13
Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.
14
Koma munachita bwino kuti munayanjana nane m'chisautso changa.
15
Koma mudziwanso inu nokha, inu Afilipi, kuti m'chiyambi cha Uthenga Wabwino, pamene ndinachoka kutuluka m'Masedoniya, sunayanjana nane Mpingo umodzi wonse m'makhalidwe a chopereka ndi cholandira, koma inu nokha;
16
pakuti m'Tesalonikanso munanditumizira pa chosowa changa kamodzi kapena kawiri.
17
Sikunena kuti nditsata choperekacho, komatu nditsata chipatso chakuchulukira ku chiwerengero chanu.
18
Koma ndili nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidachokera kwanu, mnunkho wa fundo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu.
19
Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake m'ulemerero mwa Khristu Yesu.
20
Ndipo kwa Mulungu ndi Atate wathu kukhale ulemerero kunthawi za nthawi, Amen.
21
Lankhulani woyera mtima aliyense mwa Khristu Yesu. Abalewo akukhala ndi ine alankhula inu.
22
Oyera mtima onse alankhula inu, koma makamaka iwo a banja la Kaisara.
23
Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wanu.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
All chapters:
1
2
3
4