bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Revelation 5
Revelation 5
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 6 →
1
Ndipo ndinaona m'dzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wachifumu buku lolembedwa m'kati ndi kunja kwake, losindikizika ndi zizindikiro zisanu ndi ziwiri.
2
Ndipo ndinaona mngelo wamphamvu wakulalikira ndi mau akulu, Ayenera ndani kutsegula buku, ndi kumasula zizindikiro zake?
3
Ndipo sanathe mmodzi m'Mwamba, kapena padziko, kapena pansi pa dziko kutsegula pabukupo, kapena kulipenya.
4
Ndipo ndinalira kwambiri, chifukwa sanapezedwa mmodzi woyenera kutsegula bukulo, kapena kulipenya;
5
ndipo mmodzi wa akulu ananena ndi ine, Usalire: taona, Mkango wochokera m'fuko la Yuda, Muzu wa Davide, walakika kutsegula buku ndi zizindikiro zake zisanu ndi ziwiri.
6
Ndipo ndinaona pakati pa mpando wachifumu ndi zamoyo zinai, ndi pakati pa akulu, Mwanawankhosa ali chilili ngati waphedwa; wokhala nazo nyanga zisanu ndi ziwiri, ndi maso asanu ndi awiri, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, yotumidwa ilowe m'dziko lonse.
7
Ndipo anadza, nalitenga kudzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wachifumu.
8
Ndipo pamene adatenga bukulo, zamoyo zinai ndi akulu makumi awiri mphambu anai zinagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosa, zonse zili nao azeze, ndi mbale zagolide zodzala ndi zofukiza, ndizo mapemphero a oyera mtima.
9
Ndipo aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,
10
ndipo mudawayesa iwo ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo achita ufumu padziko.
11
Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva mau a angelo ambiri pozinga mpando wachifumu, ndi zamoyo ndi akulu; ndipo mawerengedwe ao anali zikwi khumi kuchulukitsa zikwi khumi ndi zikwi za zikwi;
12
akunena ndi mau akulu, Ayenera Mwanawankhosa, wophedwayo, kulandira chilimbiko, ndi chuma, ndi nzeru, ndi mphamvu, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi chiyamiko.
13
Ndipo cholengedwa chilichonse chili m'mwamba, ndi padziko, ndi pansi pa dziko, ndi m'nyanja, ndi zonse zili momwemo, ndinazimva zilikunena, Kwa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa zikhale chiyamiko, ndi ulemu, kufikira nthawi za nthawi.
14
Ndipo zamoyo zinai zinati, Amen. Ndipo akuluwo anagwa pansi nalambira.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22