bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Ruth 3
Ruth 3
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 4 →
1
Pamenepo Naomi mpongozi wake ananena naye, Mwana wanga, kodi ndisakufunire popumulako, kuti ukhale bwino?
2
Nanga Bowazi wodziwana nafe, amene unakhala nao adzakazi ake? Taona, usiku uno apuntha barele popunthirapo.
3
Usambe tsono, nudzole, nuvale zovala zako, nutsikire popunthirapo, koma usadziwike naye munthuyo, koma atatha kudya ndi kumwa ndiko.
4
Ndipo kudzali, akagona, upenye apo ati agone, numuke, nuvundukule ku mapazi ake, nugone, ndi iyeyo adzakufotokozera zoyenera kuchita iwe.
5
Ndipo ananena naye, Zonse muzinena ndidzachita.
6
Pamenepo anatsikira popunthirapo, nachita zonse monga umo mpongozi wake adamuuza.
7
Ndipo atatha Bowazi kudya ndi kumwa, nusekerera mtima wake, anakagona kuthungo kwa mulu wa tirigu; nadza iye kachetechete, navundukula ku mapazi ake, nagona.
8
Ndipo kunali, pakati pa usiku munthuyo anadzidzimuka, natembenuka; ndipo taona pa mapazi ake pagona mkazi.
9
Nati iye, Ndiwe yani? Nayankha iye, Ndine Rute mdzakazi wanu; mufunde mdzakazi wanu chofunda chanu, pakuti inu ndinu wondiombolera cholowa.
10
Nati iye, Yehova akudalitse, mwana wanga. Chokoma chako wachichita potsiriza pano, chiposa chakuyamba chija, popeza sunatsata anyamata, angakhale osauka angakhale achuma.
11
Ndipo tsopano, mwana wanga, usaope; ndidzakuchitira zonse unenazi; pakuti onse a pa mudzi wa anthu a mtundu wanga adziwa kuti iwe ndiwe mkazi waulemu.
12
Tsopano ndipo, zoonadi, ine ndine wakukuombolera cholowa, koma pali wakukuombolera woposa ine.
13
Gona usiku uno, ndipo kudzali m'mawa, akakuombolera, chabwino, akuombolere; koma ngati safuna kukuombolera, pali Yehova, ndidzakuombolera cholowa ndine; gona mpaka m'mawa.
14
Nagona ku mapazi ake mpaka m'mawa; nalawira asanazindikirane anthu. Pakuti anati, Chisadziwike kuti mkaziyo anadza popunthirapo.
15
Ndipo anati, Bwera nacho chofunda chako, nuchigwire; nachigwira iye; ndipo anayesa miyeso isanu ndi umodzi ya barele, namsenza; atatero analowa m'mudzi.
16
Ndipo pamene anadza kwa mpongozi wake, iye anati, Wapeza bwanji, mwana wanga? Pamenepo anamfotokozera zonse anamchitira munthuyo.
17
Natinso, Miyeso, iyi isanu ndi umodzi ya barele anandipatsa, pakuti anati, Usafike kwa mpongozi wako wopanda kanthu.
18
Ndipo anati, Khala ulipo, mwana wanga, mpaka udziwa umo ukhalire mlandu; pakuti munthuyo sadzauleka mpaka atautha mlanduwo lero lino.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4