bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Zechariah 12
Zechariah 12
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 13 →
1
Katundu wa mau a Yehova wakunena Israele. Atero Yehova, wakuyala miyamba, ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kulenga mzimu wa munthu m'kati mwake;
2
Taonani, ndidzaika Yerusalemu akhale chipanda chodzandiritsa kwa mitundu yonse ya anthu yozungulirapo, ndipo chidzafikira Yuda yemwe pomangira misasa Yerusalemu.
3
Ndipo kudzachitika tsiku ilo, ndidzaika Yerusalemu akhale mwala wolemetsa mitundu yonse ya anthu; onse akuusenza adzadzilasa nao; ndi amitundu onse a pa dziko lapansi adzasonkhana kutsutsana nao.
4
Tsiku ilo, ati Yehova, ndidzakantha kavalo aliyense ndi kumdabwitsa, ndi womkwera adzayaluka; ndipo ndidzatsegulira maso anga nyumba ya Yuda, ndi kukantha kavalo aliyense wa mitundu ya anthu akhale wakhungu.
5
Ndipo akalonga a Yuda adzanena m'mtima mwao, Okhala m'Yerusalemu ndiwo mphamvu yanga m'Yehova wa makamu Mulungu wao.
6
Tsiku ilo ndidzaika akalonga a Yuda ngati phale la moto pansi pa nkhuni, ndi ngati muuni wamoto mwa mitolo ya tirigu; ndipo adzatha mitundu yonse ya anthu pozungulirapo, kudzanja lamanja ndi lamanzere; ndipo Yerusalemu adzakhalanso m'malo mwake, m'Yerusalemu.
7
Ndipo Yehova adzayamba kupulumutsa mahema a Yuda, kuti ulemerero wa nyumba ya Davide ndi ulemerero wa okhala m'Yerusalemu usakulire Yuda.
8
Tsiku ilo Yehova adzatchinjiriza okhala m'Yerusalemu; ndi iye wokhumudwa pakati pao tsiku lomwelo adzakhala ngati Davide; ndi nyumba ya Davide idzakhala ngati Mulungu, ngati mthenga wa Yehova pakati pao.
9
Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ndidzayesa kuononga amitundu onse akudza kuyambana ndi Yerusalemu.
10
Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala m'Yerusalemu, mzimu wa chisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wake mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wake woyamba.
11
Tsiku lomwelo kudzakhala maliro akulu m'Yerusalemu, ngati maliro a Hadadirimoni m'chigwa cha Megido.
12
Ndipo dziko lidzalira, banja lililonse pa lokha; banja la nyumba ya Davide pa lokha, ndi akazi ao pa okha; banja la nyumba ya Natani pa lokha, ndi akazi ao pa okha;
13
banja la nyumba ya Levi pa lokha, ndi akazi ao pa lokha; banja la Asimei pa okha, ndi akazi ao pa okha;
14
mabanja onse otsala, banja lililonse pa lokha, ndi akazi ao pa okha.
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14