bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Zephaniah 2
Zephaniah 2
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 3 →
1
Dzisanthuleni, inde santhulani; inu mtundu wosakhumba kanthu;
2
lamulo lisanabale, tsiku lisanapitirire ngati mungu, usanakugwereni mkwiyo waukali wa Yehova, lisanakugwereni tsiku la mkwiyo wa Yehova.
3
Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m'dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.
4
Pakuti Gaza adzasiyidwa, ndi Asikeloni adzakhala bwinja; adzaingitsa Asidodi usana, ndi Ekeroni adzazulidwa.
5
Tsoka, okhala m'dziko la kunyanja, mtundu wa Akereti! Mau a Yehova atsutsana nawe, Kanani, dziko la Afilisti; ndidzakuononga, kuti pasakhale wokhala m'dziko.
6
Ndipo dziko la kunyanja lidzakhala busa, ndi mapanga a abusa, ndi makola a zoweta.
7
Ndipo dziko la kunyanja lidzakhala la otsala a nyumba ya Yuda; adzadyetsa zoweta zao pamenepo; madzulo adzagona m'nyumba za Asikeloni; pakuti Yehova Mulungu wao adzawazonda, nadzabweza undende wao.
8
Ndinamva kutonza kwa Mowabu ndi matukwano a ana a Amoni, zimene anatonza nazo anthu anga, ndi kudzikuza pa malire ao.
9
Chifukwa chake, pali moyo wanga, ati Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Zedi Mowabu adzakhala ngati Sodomu, ndi ana a Amoni ngati Gomora, pochuluka khwisa ndi maenje a mchere, ndi bwinja losatha; otsala a anthu anga adzalanda zao, ndi otsala a mtundu wa anthu anga adzawalandira akhale cholowa chao.
10
Ichi adzakhala nacho m'malo mwa kudzikuza kwao, chifukwa anatonza, nadzikuza pa anthu a Yehova wa makamu.
11
Yehova adzawakhalira woopsa; pakuti adzaondetsa milungu yonse ya pa dziko lapansi; ndipo adzamlambira Iye, yense pamalo pake, a m'zisumbu zonse za amitundu.
12
Inunso Akusi, mudzaphedwa ndi lupanga langa.
13
Ndipo adzatambasulira dzanja lake kumpoto nadzaononga Asiriya, nadzasanduliza Ninive akhale bwinja, wouma ngati chipululu.
14
Ndipo zoweta zidzagona pansi pakati pake; nyama zonse za mitundumitundu; ndi vuwo ndi nungu zidzakhala m'mitu ya nsanamira zake; adzaimba mau ao m'mazenera; paziundo padzakhala chipasuko; pakuti anagadamula ntchito yake ya mkungudza.
15
Uwu ndi mudzi wosekererawo unakhala wosasamalira, unanena m'mtima mwake, Ine ndine, ndi wopanda ine palibe wina; ha! Wasanduka bwinja, mogonera nyama za kuthengo! Yense wakuupitirira adzatsonya mtsonyo, ndi kupukusa mutu.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3