bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
/
2 Chronicles 25
2 Chronicles 25
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 26 →
1
Amaziya anali wa zaka 25 pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 29. Dzina la amayi ake linali Yehoyadini wa ku Yerusalemu.
2
Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova, koma osati ndi mtima wonse.
3
Pamene mphamvu zonse zaufumu zinali mʼmanja mwake, iye anapha akuluakulu amene anapha abambo ake, mfumu ija.
4
Komabe iye sanaphe ana awo koma anatsatira zolembedwa mʼbuku la Mose, mʼmene Yehova analamula kuti, “Makolo sadzaphedwa chifukwa cha ana awo kapena ana kuphedwa chifukwa cha makolo awo. Aliyense adzafera machimo ake.”
5
Amaziya anasonkhanitsa anthu a ku Yuda ndipo anawapatsa zochita molingana ndi mabanja awo kukhala anthu olamulira 1,000, ndi olamulira 100 pa Ayuda onse ndi Benjamini. Ndipo iye anawerenga amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirirapo napeza kuti analipo amuna 300,000 okonzeka kugwira ntchito ya usilikali, okhoza kugwiritsa ntchito mkondo ndi chishango.
6
Iye analembanso ntchito anthu odziwa nkhondo 100,000 ochokera ku Israeli pa mtengo wa makilogalamu 3,400 a siliva.
7
Koma munthu wa Mulungu anabwera kwa iye ndipo anati, “Inu mfumu, asilikali awa ochokera ku Israeli asapite ndi inu, pakuti Yehova sali ndi Israeli kapena ndi aliyense wa anthu a Efereimu.
8
Ngakhale mupite ndi kuchita nkhondo molimba mtima, Mulungu adzakugonjetsani pamaso pa adani anu, pakuti Mulungu ali ndi mphamvu yothandiza kapena kugonjetsa.”
9
Amaziya anafunsa munthu wa Mulungu kuti, “Koma nanga za makilogalamu aja a siliva amene ndapereka kwa asilikali a Israeli?” Munthu wa Mulungu anayankha kuti, “Yehova atha kukupatsani zambiri kuposa zimenezo.”
10
Choncho Amaziya anachotsa asilikali amene anabwera kwa iye kuchokera ku Efereimu ndipo anawatumiza kwawo. Iwo anakwiyira anthu a ku Yuda ndipo anapita kwawo atapsa mtima kwambiri.
11
Ndipo Amaziya analimba mtima ndipo anatsogolera gulu lake lankhondo ku Chigwa cha Mchere, kumene anapha anthu 10,000 a ku Seiri.
12
Gulu la ankhondo la Yuda linagwiranso anthu amoyo 10,000, napita nawo pamwamba pa thanthwe ndipo anawaponya pansi kotero kuti onse ananyenyeka.
13
Pa nthawi imeneyi asilikali amene Amaziya anawabweza ndipo sanawalole kuti achite nawo nkhondo, anakathira nkhondo mizinda ya Yuda kuyambira ku Samariya mpaka ku Beti-Horoni. Iwo anapha anthu 3,000 ndipo anafunkha katundu wambiri.
14
Amaziya atabwerera kuja anakapha Aedomu, anabweretsa milungu ya anthu a ku Seiri. Ndipo anayika kuti ikhale milungu yake, ankayipembedza ndi kupereka nsembe zopsereza.
15
Yehova anakwiyira Amaziya, ndipo anamutumizira mneneri amene anati, “Nʼchifukwa chiyani mukupembedza milungu ya anthu awa, imene sinathe kupulumutsa anthu ake mʼdzanja lanu?”
16
Iye ali kuyankhula, mfumu inati, “Kodi ife takusankha iwe kuti ukhale mlangizi wa mfumu? Khala chete! Ufuna kuphedweranji?” Choncho mneneriyo analeka koma anati, “Ine ndikudziwa kuti Mulungu watsimikiza kukuwonongani chifukwa mwachita izi ndipo simunamvere uphungu wanga.”
17
Amaziya mfumu ya ku Yuda, atafunsa alangizi ake, anatumiza mawu awa kwa Yowasi mwana wa Yehowahazi mwana wa Yehu, mfumu ya Israeli: “Bwera udzakumane nane maso ndi maso.”
18
Koma Yowasi mfumu ya Israeli inayankha Amaziya mfumu ya Yuda kuti, “Nthawi ina kamtengo kaminga ka ku Lebanoni kanatumiza mawu kwa mkungudza wa ku Lebanoni kuti, ‘Pereka mwana wako wamkazi kwa mwana wanga kuti amukwatire!’ Koma chirombo cha ku Lebanoni chinabwera ndi kupondaponda mtengo wa minga uja.
19
Iwe ukuti wagonjetsa Edomu, ndipo tsopano ukudzikuza ndi kudzitamandira, koma khala kwanu komweko! Nʼchifukwa chiyani ukufuna mavuto ndi kudzichititsa kuti ugwe pamodzinso ndi Yuda?”
20
Komabe Amaziya sanamvere pakuti ndi Mulungu amene anakonzeratu kuti awapereke kwa Yehowasi, chifukwa iwo amapembedza milungu ya ku Edomu.
21
Kotero Yowasi mfumu ya Israeli inakamuthira nkhondo. Iye ndi Amaziya anayangʼanana maso ndi maso ku Beti-Semesi ku Yuda.
22
Yuda anagonjetsedwa ndi Israeli ndipo munthu aliyense anathawira kwawo.
23
Yehowahazi mfumu ya Israeli inagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yowasi, mwana wa Ahaziya ku Beti-Semesi. Yehowasi anabwera naye ku Yerusalemu ndipo anagwetsa khoma la Yerusalemu kuyambira pa Chipata cha Efereimu mpaka ku Chipata Chapangodya, khoma lotalika mamita 180.
24
Iye anatenga golide ndi siliva yense ndi zida zonse zimene zimapezeka mʼNyumba ya Mulungu zimene ankazisamalira Obedi-Edomu, pamodzinso ndi chuma cha mʼnyumba yaufumu ndipo anatenga anthu ngati chikole.
25
Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda anakhala ndi moyo kwa zaka khumi ndi zisanu atamwalira Yehowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya Israeli.
26
Ntchito zina za mfumu Amaziya, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mafumu a Yuda ndi Israeli?
27
Kuyambira nthawi imene Amaziya analeka kutsatira Yehova anthu anamukonzera chiwembu mu Yerusalemu ndipo anathawira ku Lakisi, koma adaniwo anatumiza anthu ku Lakisiko ndipo anamupha komweko.
28
Iwo anabwera naye ali pa kavalo ndipo anayikidwa mʼmanda ndi makolo ake mu mzinda wa Yuda.
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 26 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36