bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
/
Acts 25
Acts 25
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 26 →
1
Patapita masiku atatu Festo atafika mʼdera lake, anachoka ku Kaisareya ndi kupita ku Yerusalemu.
2
Kumeneko akulu a ansembe ndi atsogoleri a Chiyuda anabwera kwa iye ndi kumufotokozera mlandu wa Paulo.
3
Iwo anamupempha Festo kuti awakomere mtima potumiza Paulo ku Yerusalemu, pakuti anali atakonzekera chiwembu kuti amuphe Pauloyo pa njira.
4
Festo anayankha kuti, “Paulo akusungidwa ku Kaisareya, ndipo ndipita kumeneko posachedwa.
5
Ena mwa atsogoleri anu apite nane kumeneko, kuti akafotokoze mlandu wa munthuyu, ngati anachita kanthu kalikonse kolakwika.”
6
Festo atakhala nawo masiku asanu ndi atatu kapena khumi iye anapita ku Kaisareya, ndipo mmawa mwake anayitanitsa bwalo nalamula kuti abweretse Paulo pamaso pake.
7
Paulo atafika, Ayuda amene anafika kuchokera ku Yerusalemu anayima momuzungulira. Iwo anamunenera zinthu zoopsa zambiri zimene sakanatha kubweretsa umboni wake.
8
Kenaka Paulo ananena mawu ake odziteteza kuti, “Ine sindinalakwirepo lamulo la Ayuda, kapena Nyumba ya Mulungu kapenanso Kaisara.”
9
Festo, pofuna kuti Ayuda amukonde anafunsa Paulo kuti, “Kodi iwe ukufuna kupita ku Yerusalemu, kuti kumeneko ukafotokoze mlandu wako pamaso panga?”
10
Paulo anayankha kuti, “Ine tsopano ndayima pamaso pa bwalo la milandu la Kaisara, ndiko kumene ayenera kundiweruza. Ine sindinalakwire Ayuda, monga inu mukudziwa bwino.
11
Koma ngati ndili wolakwa, ngati ndachita kanthu koyenera kuphedwa, ine sindikukana kufa. Koma ngati mlandu umene abweretsa Ayudawa siwoona, palibe munthu angathe kundipereka mʼmanja mwawo. Ndikupempha kuti ndikaweruzidwe ndi Kaisara!”
12
Festo atakambirana ndi akuluakulu abwalo lake, anati, “Popeza wapempha kupita kwa Kaisara, kwa Kaisara udzapitadi!”
13
Patapita masiku ochepa mfumu Agripa pamodzi ndi Bernisi anabwera ku Kaisareya kudzalonjera Festo.
14
Atakhala kumeneko masiku angapo, Festo anafotokozera mfumuyo za mlandu wa Paulo. Iye anati, “Kuli munthu wina kuno amene Felike anamusiya mʼndende.
15
Nditapita ku Yerusalemu akulu a ansembe ndi akuluakulu a Ayuda anandifotokozera mlandu wake ndipo anandipempha kuti ndigamule kuti ndi wolakwa.
16
“Ine ndinawayankha kuti si mwambo wa Aroma kungomupereka munthu ayi. Munthu woyimbidwa mlanduyo amayenera kukumana nawo omunenezawo, kuti iye akhale ndi mwayi woyankhapo pa zimene akumuyimba mlanduzo.
17
Atabwera kuno pamodzi ndi ine, sindinachedwetse mlanduwo, koma ndinayitanitsa bwalo mmawa mwake ndi kulamula kuti amubweretse munthuyo.
18
Omuyimba mlandu aja atayimirira kuti ayankhule, iwo sananene cholakwa chilichonse chimene ndimayembekezera.
19
Mʼmalo mwake, anatsutsana naye pa fundo zina za chipembedzo chawo ndi za munthu wakufa, dzina lake Yesu, amene Paulo akuti ali moyo.
20
Ine ndinathedwa nzeru wosadziwa momwe ndikanafufuzira nkhaniyi; kotero ndinafunsa ngati akanafuna kupita ku Yerusalemu kuti akaweruzidwe kumeneko.
21
Koma Paulo anapempha kuti akaonekere pamaso pa mfumu ya Chiroma, ndipo ndinalamula kuti asungidwe mpaka pamene ndidzamutumize kwa Kaisara.”
22
Ndipo Agripa anati kwa Festo, “Ine ndikufuna ndimumve ndekha munthu ameneyu.” Iye anayankha kuti, “Mudzamumva mawa.”
23
Mmawa mwake Agripa ndi Bernisi anabwera mwaulemu waukulu waufumu nalowa mʼbwalo la milandu pamodzi ndi akulu a asilikali ndiponso akuluakulu a mu mzindawo. Atalamula Festo kuti Paulo abwere, anabweradi.
24
Festo anati, “Mfumu Agripa, ndi onse amene muli nafe pano, mukumuona munthu uyu! Ayuda onse anandipempha ine za uyu ku Yerusalemu ndiponso kuno ku Kaisareya, mofuwula kuti, ameneyu sayenera kukhala ndi moyo.
25
Ine ndinapeza kuti iyeyu sanachite kanthu koyenera kufa, koma popeza anapempha kuti apite kwa mfumu ya Chiroma, ine ndinatsimikiza zomutumiza ku Roma.
26
Koma ndilibe kanthu kenikeni koti ndilembere Wolemekezekayo za iyeyu. Nʼchifukwa chake ndabwera naye pamaso pa nonsenu, makamaka kwa inuyo mfumu Agripa, kuti mwina mukamufunsitsa ndikhale ndi choti ndilembe.
27
Pakuti ine ndikuganiza kuti ndi chinthu chopanda nzeru kutumiza wamʼndende popanda kutchula zifukwa zenizeni za mlandu wake.”
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 26 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28