bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
/
Ezekiel 31
Ezekiel 31
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 32 →
1
Pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu, chaka cha khumi ndi chimodzi, Yehova anandiyankhula kuti:
2
“Iwe mwana wa munthu, unene kwa Farao mfumu ya Igupto ndi gulu lake lankhondo. Awawuze kuti, “ ‘Kodi mu ukulu wanu ndani angafanane ndi inu?
3
Taonani, ndidzakufanizirani ndi mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni, wa nthambi zokongola zochititsa mthunzi mʼnkhalango. Unali wautali, msonga zake zooneka pamwamba pa nkhalango.
4
Madzi ndiwo ankawukulitsa mkungudzawo, akasupe ozama ankawutalikitsa. Mitsinje yake inkayenda mozungulira malo amene unaliwo ndipo ngalande zake zinkafika ku mitengo yonse ya mʼmunda.
5
Choncho unatalika kwambiri kupambana mitengo yonse ya mʼmunda. Nthambi zake zinachuluka ndi kutalika kwambiri, chifukwa inkalandira madzi ambiri.
6
Mbalame zonse zamlengalenga zinkamanga zisa zake mʼnthambi za mtengowo. Nyama zakuthengo zonse zinkaswanirana mʼmunsi mwa nthambi zake. Mitundu yotchuka ya anthu inkakhala mu mthunzi wake.
7
Unali wokongola kwambiri, wa nthambi zake zotambalala, chifukwa mizu yake inazama pansi kumene kunali madzi ochuluka.
8
Mʼmunda wa Mulungu munalibe mkungudza wofanana nawo, kapena mitengo ya payini ya nthambi zofanafana ndi nthambi zake. Munalibenso mtengo wa mkuyu nthambi zofanafana ndi zake. Mʼmunda wa Mulungu munalibe mtengo wina uliwonse wofanana ndi iwo kukongola kwake.
9
Ine ndinawupanga wokongola wa nthambi zochuluka. Mitengo yonse ya mu Edeni, mʼmunda wa Mulungu inawuchitira nsanje.
10
“ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Chifukwa kuti mtengowo unatalika kwambiri, unatulutsa songa zake mpaka ku thambo, ndipo unadzikweza chifukwa cha msinkhu wake,
11
ndinawupereka mʼdzanja la mfumu ya mitundu ya anthu kuti awulange molingana ndi kuyipa kwake.
12
Anthu ankhanza kwambiri amitundu ya anthu achilendo adzawudula ndi kuwusiya. Nthambi zake zidzagwera pa mapiri ndi mu zigwa zonse. Nthambi zake zidzathyokera mʼmitsinje ya mʼdzikomo. Motero mitundu yonse ya anthu a dziko lapansi amene ankasangalala mu mthunzi wake idzawusiya.
13
Mbalame zonse zamlengalenga zidzakhala pa mtengo wakugwawo, ndipo nyama zakuthengo zonse zidzakhala pa nthambi zake.
14
Zidzakutero kuti pasakhalenso mitengo inanso ya mʼmbali mwa madzi yotalika kwambiri, imene idzatalike kwambiri ndi songa zake kufika mpaka ku mitambo. Komanso kuti pasadzakhalenso mitengo yolandira bwino madzi, imene idzatalika motero. Paja yonseyo kutha kwake ndi kufa, kupita ku dziko lapansi kukhala ndi anthu akufa amene analowa mʼmanda kale.
15
“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa nthawi imene mkungudzawo unatsikira ku manda, ndinawuza nyanja kuti iwulire maliro pakuwuphimba. Ndinawumitsa mitsinje ndipo madzi ambiri anaphwa. Ndinabweretsa mdima pa Lebanoni chifukwa cha mtengowo ndipo mitengo yonse ya mʼdzikomo inawuma.
16
Mitundu ya anthu inagwedezeka pakumva mkokomo wa kugwa kwake, pamene ndinawutsitsira ku manda pamodzi ndi iwo amene anafa. Pamenepo ku dziko la akufa mitengo yonse ya ku Edeni pamodzi ndi ya ku Lebanoni yosankhidwa bwino inasangalatsidwa chifukwa cha zimenezi.
17
Amene ankakhala mu mthunzi wake, amene ankayanjana nawo, iwonso anapita nawo pamodzi ku manda, kukakhala pamodzi ndi amene anaphedwa ndi lupanga pakati pa mitundu ya anthu.
18
“ ‘Ndi mitengo iti ya mu Edeni imene ingafanane ndi kukongola kwako ndi ulemerero wako? Komabe iwenso, udzatsikira ku dziko la anthu akufa pamodzi ndi mitengo ya mu Edeni. Udzagona pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, anthu amene anaphedwa pa nkhondo. “ ‘Mtengowo ndi Farao ndi gulu lake lankhondo, akutero Ambuye Yehova.’ ”
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 32 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48