bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
/
Ezra 2
Ezra 2
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 3 →
1
Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerako ku ukapolo, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anawagwira ukapolo ndi kupita nawo ku Babuloni (iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wake.
2
Iwo anabwerera pamodzi ndi Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Seruya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu ndi Baana). Chiwerengero cha anthu aamuna a Israeli chinali chotere:
3
Zidzukulu za Parosi — 2,172
4
zidzukulu za Sefatiya — 372
5
zidzukulu za Ara — 775
6
zidzukulu za Pahati-Mowabu (zochokera kwa Yesuwa ndi Yowabu) — 2,812
7
zidzukulu za Elamu — 1,254
8
zidzukulu za Zatu — 945
9
zidzukulu za Zakai — 760
10
zidzukulu za Bani — 642
11
zidzukulu za Bebai — 623
12
zidzukulu za Azigadi — 1,222
13
zidzukulu za Adonikamu — 666
14
zidzukulu za Bigivai — 2,056
15
zidzukulu za Adini — 454
16
zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya) — 98
17
zidzukulu za Bezayi — 323
18
zidzukulu za Yora — 112
19
zidzukulu za Hasumu — 223
20
zidzukulu za Gibari — 95.
21
Anthu a ku Betelehemu — 123
22
Anthu aamuna a ku Netofa — 56
23
Anthu aamuna a ku Anatoti — 128
24
Anthu aamuna a ku Azimaveti — 42
25
Anthu aamuna a ku Kiriati Yearimu, Kefira ndi Beeroti — 743
26
Anthu aamuna a ku Rama ndi Geba — 621
27
Anthu aamuna a ku Mikimasi — 122
28
Anthu aamuna a ku Beteli ndi Ai — 223
29
Anthu aamuna a ku Nebo — 52
30
Anthu aamuna a ku Magaibisi — 156
31
Anthu aamuna a ku Elamu wina — 1,254
32
Anthu aamuna a ku Harimu — 320
33
Anthu aamuna a ku Lodi, Hadidi ndi Ono — 725
34
Anthu aamuna a ku Yeriko — 345
35
Anthu aamuna a ku Sena — 3,630.
36
Ansembe anali awa: Zidzukulu za Yedaya (kudzera mu banja la Yesuwa) — 973
37
Zidzukulu za Imeri — 1,052
38
Zidzukulu za Pasuri — 1,247
39
Zidzukulu za Harimu — 1,017.
40
Alevi anali awa: Zidzukulu za Yesuwa ndi Kadimieli (kudzera mwa ana a Hodaviya) — 74.
41
Anthu oyimba nyimbo anali awa: Zidzukulu za Asafu — 128.
42
Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa: Zidzukulu za Salumu, zidzukulu za Ateri, zidzukulu za Talimoni, zidzukulu za Akubu, zidzukulu za Hatita ndi zidzukulu za Sobai — 139.
43
Otumikira ku Nyumba ya Mulungu anali awa: Zidzukulu za Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti,
44
zidzukulu za Kerosi, zidzukulu za Siyaha, Padoni,
45
zidzukulu za Lebana, zidzukulu za Hagaba, zidzukulu za Akubu,
46
zidzukulu za Hagabu, zidzukulu za Salimayi, zidzukulu za Hanani,
47
zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari, zidzukulu za Reaya,
48
zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nekoda, zidzukulu za Gazamu,
49
zidzukulu za Uza, zidzukulu za Peseya, zidzukulu za Besai,
50
zidzukulu za Asina, zidzukulu za Meunimu, Nefusimu,
51
zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri,
52
zidzukulu za Baziruti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa,
53
zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema,
54
zidzukulu za Neziya ndi zidzukulu za Hatifa.
55
Zidzukulu za antchito a Solomoni zinali izi: Zidzukulu za Sotai, zidzukulu za Hasofereti, zidzukulu za Peruda,
56
zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli,
57
zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu, zidzukulu za Pokereti, Hazebayimu ndi Ami.
58
Chiwerengero cha onse otumikira ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za Solomoni chinali — 392.
59
Anthu ali mʼmunsiwa anabwera kuchokera ku mizinda ya Teli-Mela, Teli-Harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, ngakhale samatha kutsimikiza kuti mafuko awo analidi Aisraeli enieni kapena ayi:
60
Zidzukulu za Delaya, zidzukulu za Tobiya, ndi zidzukulu za Nekoda. Onse pamodzi anali — 652.
61
Ndi ena pakati pa ansembe anali awa: Zidzukulu za Hobiya, Hakozi, ndi Barizilai (Zidzukulu za Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai. Barizilai ameneyu ndi uja anakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi ndipo ankadziwika ndi dzina la bambo wawoyo.)
62
Amenewa anafufuza mayina awo mʼbuku lofotokoza mbiri ya mafuko awo, koma mayinawo sanawapezemo, choncho anawachotsa pa unsembe ngati anthu odetsedwa pa zachipembedzo.
63
Bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo mpaka atapezeka wansembe wodziwa kuwombeza ndi Urimu ndi Tumimu.
64
Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 42,360,
65
kuwonjezera pamenepo, panalinso antchito awo aamuna ndi aakazi okwanira 7,337. Analinso ndi amuna ndi akazi oyimba nyimbo okwanira 200.
66
Anali ndi akavalo 736, nyulu 245,
67
ngamira 435 ndi abulu 6,720.
68
Atafika ku Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu, ena mwa atsogoleri a mabanja anapereka zopereka zaufulu zothandizira kumanganso Nyumba ya Mulungu pamalo pake pakale.
69
Anapereka kwa msungichuma wa ntchitoyo molingana ndi mmene aliyense chuma chake chinalili: golide wa makilogalamu 500, siliva makilogalamu 2,800 ndi zovala za ansembe zokwanira 100.
70
Ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda ndi antchito a ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmidzi ya makolo awo.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10