bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
/
Hebrews 5
Hebrews 5
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 6 →
1
Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa kuchokera pakati pa anthu ndipo amayikidwa kuti aziwayimirira pamaso pa Mulungu, kuti azipereka mphatso ndi nsembe chifukwa cha machimo.
2
Popeza kuti iye mwini ali ndi zofowoka zake, amatha kuwalezera mtima amene ali osadziwa ndi osochera.
3
Chifukwa cha ichi, iye amadziperekera nsembe chifukwa cha machimo ake omwe ndiponso chifukwa cha machimo a anthu ena.
4
Palibe amene amadzipatsa yekha ulemu wotere, koma amachita kuyitanidwa ndi Mulungu monga momwe anayitanidwira Aaroni.
5
Nʼchifukwa chake Khristu sanadzipatse yekha ulemu wokhala Mkulu wa ansembe. Koma Mulungu anamuwuza kuti, “Iwe ndiwe Mwana wanga; Ine lero ndakhala Atate ako.”
6
Ndipo penanso anati, “Iwe ndiwe wansembe mpaka muyaya, monga mwa unsembe wa Melikizedeki.”
7
Yesu, pa nthawi imene anali munthu pa dziko lapansi pano, anapereka mapemphero ake ndi zopempha mofuwula ndi misozi kwa Iye amene akanamupulumutsa ku imfa, ndipo anamumvera chifukwa anagonjera modzipereka.
8
Ngakhale Iye anali Mwana wa Mulungu anaphunzira kumvera pomva zowawa.
9
Atasanduka wangwiro kotheratu, anakhala gwero la chipulumutso chosatha kwa onse omvera Iye.
10
Ndipo Mulungu anamuyika kukhala Mkulu wa ansembe, monga mwa dongosolo la unsembe wa Melikizedeki.
11
Tili ndi zambiri zoti tinganene pa zimenezi, koma ndi zovuta kukufotokozerani chifukwa ndinu ochedwa kuphunzira.
12
Ngakhale kuti pa nthawi ino munayenera kukhala aphunzitsi, pakufunikabe munthu wina kuti abwerezenso kudzakuphunzitsani maphunziro oyambira a choonadi cha Mulungu. Ndinu ofunika mkaka osati chakudya cholimba!
13
Aliyense amene amangodya mkaka okha, akanali mwana wakhanda, sakudziwa bwino chiphunzitso cha chilungamo.
14
Koma chakudya cholimba ndi cha anthu okhwima msinkhu, amene pogwiritsa ntchito nzeru zawo, aphunzira kusiyanitsa chabwino ndi choyipa.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13