bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
/
Hosea 9
Hosea 9
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 10 →
1
Iwe Israeli, usakondwere; monga imachitira mitundu ina. Pakuti wakhala wosakhulupirika kwa Mulungu wako; umakonda malipiro a chiwerewere pa malo aliwonse opunthira tirigu.
2
Malo opunthira tirigu ndi malo opsinyira mphesa sadzadyetsa anthu; adzasowa vinyo watsopano.
3
Sadzakhalanso mʼdziko la Yehova. Efereimu adzabwerera ku Igupto ndipo mudzadya chakudya chodetsedwa ku Asiriya.
4
Iwo sadzaperekanso chopereka cha chakumwa kwa Yehova, kapena nsembe zawo kuti akondweretse Yehovayo. Nsembe zotere zidzakhala kwa iwo ngati chakudya cha anamfedwa; onse akudya chakudya chimenechi adzakhala odetsedwa. Chakudya ichi chidzakhala chodya okha, sichidzalowa mʼnyumba ya Yehova.
5
Kodi mudzachita chiyani pa tsiku la maphwando anu oyikika; pa masiku a zikondwerero za Yehova?
6
Ngakhale iwo atathawa chiwonongeko, Igupto adzawasonkhanitsa, ndipo Mefisi adzawayika mʼmanda. Khwisa adzamera pa ziwiya zawo zasiliva, ndipo minga idzamera mʼmatenti awo.
7
Masiku achilango akubwera, masiku obwezera ali pafupi. Israeli adziwe zimenezi. Chifukwa machimo anu ndi ochuluka kwambiri ndipo udani wanu pa Mulungu ndi waukulu kwambiri. Mneneri amamuyesa chitsiru, munthu wanzeru za kwa Mulungu ngati wamisala.
8
Mneneri pamodzi ndi Mulungu wanga ndiwo alonda a Efereimu, koma mneneri amutchera misampha mʼnjira zake zonse, ndipo udani ukumudikira mʼnyumba ya Mulungu wake.
9
Iwo azama mu zachinyengo monga masiku a Gibeya. Mulungu adzakumbukira zolakwa zawo ndipo adzawalanga chifukwa cha machimo awo.
10
“Pamene ndinamupeza Israeli zinali ngati kupeza mphesa mʼchipululu. Nditaona makolo anu, zinali ngati ndikuona nkhuyu zoyambirira kupsa. Koma atafika ku Baala Peori, anadzipereka ku fano lija lochititsa manyazi ndipo anakhala onyansa ngati chinthu chimene anachikondacho.
11
Ulemerero wa Efereimu udzawuluka ngati mbalame. Sipadzakhalanso kubereka ana, kuyembekezera kapena kutenga pathupi.
12
Ngakhale atalera ana ndidzachititsa kuti mwana aliyense amwalire. Tsoka kwa anthuwo pamene Ine ndidzawafulatira!
13
Ndaona Efereimu ngati Turo, atadzalidwa pa nthaka ya chonde. Koma Efereimu adzatsogolera ana ake kuti akaphedwe.”
14
Inu Yehova, muwapatse. Kodi mudzawapatsa chiyani? Apatseni mimba yomangopita padera ndi mawere owuma.
15
“Chifukwa cha zoyipa zawo zonse ku Giligala, Ine ndinawada kumeneko. Chifukwa cha machitidwe awo auchimo, ndidzawapirikitsa mʼnyumba yanga. Sindidzawakondanso; atsogoleri awo onse ndi owukira.
16
Efereimu wathedwa, mizu yake yauma sakubalanso zipatso. Ngakhale atabereka ana, Ine ndidzapha ana awo okondedwawo.”
17
Mulungu wanga adzawakana chifukwa sanamumvere Iye; adzakhala oyendayenda pakati pa anthu a mitundu ina.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14