bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
/
Nahum 2
Nahum 2
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 3 →
1
Wodzathira nkhondo akubwera kudzalimbana nawe, Ninive. Tetezani malinga anu, dziyangʼanani ku msewu, konzekerani nkhondo, valani dzilimbe.
2
Yehova adzabwezeretsa ulemerero wa Yakobo ngati ulemerero wa Israeli, ngakhale anthu owononga anawawononga kotheratu ndipo anawononganso mpesa wawo.
3
Zishango za ankhondo ake ndi zofiira; asilikali ake avala zovala zofiirira. Zitsulo za pa magaleta zikunyezimira tsiku la kukonzekera kwake. Akuonetsa mikondo ya mkungudza yonoledwa.
4
Magaleta akuthamanga mʼmisewu akungothamangathamanga pa mabwalo. Akuoneka ngati miyuni yoyaka; akuthamanga ngati chingʼaningʼani.
5
Iye akuyitanitsa asilikali ake wolemekezeka, koma iwo akubwera napunthwa. Akuthamangira ku linga la mzinda; akuyimika chodzitchinjirizira pamalo pake.
6
Atsekula zipata zotchinga madzi a mu mtsinje ndipo nyumba yaufumu yagwa.
7
Zatsimikizika kuti mzinda utengedwa ndi kupita ku ukapolo. Akapolo aakazi akulira ngati nkhunda ndipo akudziguguda pachifuwa.
8
Ninive ali ngati dziwe, ndipo madzi ake akutayika. Iwo akufuwula kuti, “Imani! Imani!” Koma palibe amene akubwerera.
9
Funkhani siliva! Funkhani golide! Katundu wake ndi wochuluka kwambiri, chuma chochokera pa zinthu zake zamtengowapatali!
10
Iye wawonongedwa, wafunkhidwa ndipo wavulidwa! Mitima yasweka, mawondo akuwombana, anthu akunjenjemera ndipo nkhope zasandulika ndi mantha.
11
Kodi tsopano dzenje la mikango lili kuti, malo amene mikango inkadyetserako ana ake, kumene mkango waumuna ndi waukazi unkapitako, ndipo ana a mkango sankaopa kanthu kalikonse?
12
Mkango waumuna unkapha nyama yokwanira ana ake ndiponso kuphera nyama mkango waukazi, kudzaza phanga lake ndi zimene wapha ndiponso dzenje lake ndi nyama imene waphayo.
13
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ine ndikutsutsana nawe. Ndidzatentha magaleta ako mpaka utsi tolotolo, ndipo lupanga lidzapha mikango yako yayingʼono; sindidzakusiyira chilichonse choti udye pa dziko lapansi. Mawu a amithenga anu sadzamvekanso.”
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3