bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
/
Nehemiah 7
Nehemiah 7
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 8 →
1
Khoma linamangidwa ndipo zitseko zinayikidwa. Pambuyo pake alonda a Nyumba ya Mulungu, oyimba nyimbo ndiponso Alevi anasankhidwa.
2
Kenaka ine ndinasankha mʼbale wanga Hanani pamodzi ndi Hananiya woyangʼanira nsanja yankhondo kukhala olamulira Yerusalemu chifukwa iyeyu anali munthu odalirika ndi woopa Mulungu kuposa anthu ena.
3
Ine ndinawawuza kuti, “Musalole kuti zipata za Yerusalemu zitsekulidwe mpaka dzuwa litatentha, ndipo alonda asanaweruke aonetsetse kuti atseka zitseko ndi kuzipiringidza. Musankhe alonda pakati pa anthu okhala mu Yerusalemu, ena akhale pa malo pawo ndi ena akhale moyangʼanana ndi nyumba zawo.”
4
Tsono mzinda wa Yerusalemu unali wotambasuka ndiponso waukulu koma munali anthu ochepa ndipo nyumba zinali zisanamangidwe.
5
Ndipo Mulungu wanga anayika mu mtima mwanga maganizo oti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, akuluakulu ndi anthu onse kuti alembetse mayina mwa mabanja awo. Ndinapeza buku limene munalembedwa mayina a mabanja a iwo amene anayamba kubwera kuchokera ku ukapolo. Izi ndi zimene ndinazipeza zitalembedwa mʼmenemo:
6
Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerera kuchokera ku ukapolo amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawatenga ukapolo. Iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake.
7
Anabwera pamodzi ndi atsogoleri awa: Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu ndi Baana. Tsono chiwerengero cha anthu a ku Israeli chinali chotere:
8
Zidzukulu za Parosi — 2,172
9
Zidzukulu za Sefatiya — 372
10
Zidzukulu za Ara — 652
11
Zidzukulu za Pahati-Mowabu (kudzera mu mʼbado wa Yesuwa ndi Yowabu) — 2,818
12
Zidzukulu za Elamu — 1,254
13
Zidzukulu za Zatu — 845
14
Zidzukulu za Zakai — 760
15
Zidzukulu za Binuyi — 648
16
Zidzukulu za Bebai — 628
17
Zidzukulu za Azigadi — 2,322
18
Zidzukulu za Adonikamu — 667
19
Zidzukulu za Abigivai — 2,067
20
Zidzukulu za Adini — 655
21
Zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya) — 98
22
Zidzukulu za Hasumu — 328
23
Zidzukulu za Bezayi — 324
24
Zidzukulu za Harifu — 112
25
Zidzukulu za Gibiyoni — 95.
26
Anthu a ku Betelehemu ndi Netofa — 188
27
Anthu a ku Anatoti — 128
28
Anthu a ku Beti-Azimaveti — 42
29
Anthu a ku Kiriati Yeyarimu Kefira ndi Beeroti — 743
30
Anthu a ku Rama ndi Geba — 621
31
Anthu a ku Mikimasi — 122
32
Anthu a ku Beteli ndi Ai — 123
33
Anthu a ku Nebo winayo — 52
34
Ana a Elamu wina — 1,254
35
Zidzukulu za Harimu — 320
36
Zidzukulu za Yeriko — 345
37
Zidzukulu za Lodi, Hadidi ndi Ono — 721
38
Zidzukulu za Senaya — 3,930.
39
Ansembe anali awa: A banja la Yedaya (ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa) — 973
40
Zidzukulu za Imeri — 1,052
41
Zidzukulu za Pasi-Huri — 1,247
42
Zidzukulu za Harimu — 1,017.
43
Alevi anali awa: A banja la Yesuwa ndi Kadimieli, ndiye kuti zidzukulu za Hodaviya — 74.
44
Anthu oyimba: Zidzukulu za Asafu — 148.
45
Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa: Zidzukulu za Salumu, Ateri, Talimoni, Hatita ndi Sobai — 138.
46
Anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu anali awa: Zidzukulu za Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti,
47
Zidzukulu Kerosi, zidzukulu za Siya, zidzukulu za Padoni
48
Zidzukulu za Lebana za Hagaba, ndi za Salimayi,
49
Zidzukulu za Hanani, zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari,
50
Zidzukulu za Reyaya, zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nehoda,
51
Zidzukulu za Gazamu, zidzukulu za Uza, zidzukulu za Paseya,
52
Zidzukulu za Besai, zidzukulu za Meunimu, zidzukulu za Nefusimu,
53
Zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri,
54
Zidzukulu za Baziliti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa,
55
Zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema
56
Zidzukulu za Neziya, ndi zidzukulu za Hatifa.
57
Zidzukulu za antchito a Solomoni: Zidzukulu za Sotai, zidzukulu za Sofereti, zidzukulu za Perida
58
zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli,
59
zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu zidzukulu za Pokereti-Hazebaimu ndi zidzukulu Amoni.
60
Anthu onse ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za antchito a Solomoni analipo — 392.
61
Ali munsiwa anachokera ku Teli-Mela, Teri-Harisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, koma sanathe kunena mwa tchutchutchu kuti makolo awo kapena mafuko awo analidi Aisraeli kapena ayi.
62
Zidzukulu za Delaya, zidzukulu za Tobiya ndi zidzukulu za Nekoda — 642.
63
Ndiponso ena pakati pa ansembe anali awa: zidzukulu za Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai (munthu amene anakwatira mwana wamkazi wa Barizilai wa ku Giliyadi ndipo amatchedwa dzina limenelo).
64
Iwowa anafufuzafufuza mayina awo mʼbuku la mibado ya mabanja awo ndipo sanapeze mayina awo kotero anachotsedwa pa unsembe nawerengedwa ngati odetsedwa pa chipembedzo.
65
Choncho bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo chakudya china chilichonse choperekedwa kwa Mulungu mpaka patapezeka wansembe wodziwa kugwiritsa bwino ntchito ya Urimu ndi Tumimu.
66
Chiwerengero chonse cha anthuwa chinali 42,360.
67
Kuwonjezera pamenepa panali antchito awo aamuna ndi aakazi 7,337 ndiponso anthu aamuna ndi aakazi oyimba nyimbo okwanira 245.
68
Panali akavalo 736, abulu angʼonoangʼono 245.
69
Ngamira zawo zinalipo 435 ndipo abulu analipo 6,720.
70
Atsogoleri ena a mabanja anapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa anapereka ku thumba losungira chuma, ndalama zagolide za makilogalamu asanu ndi atatu, mabeseni makumi asanu ndi zovala za ansembe 530.
71
Atsogoleri ena amabanja anapereka ku thumba losungira chuma ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndiponso ndalama za siliva zokwana makilogalamu 1,250.
72
Anthu ena onse otsala anapereka ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndalama za siliva zokwana makilogalamu 140, ndiponso zovala za ansembe 67.
73
Choncho ansembe, Alevi, alonda a Nyumba ya Mulungu, anthu oyimba nyimbo, ena mwa anthu wamba, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmizinda yawo. Pofika mwezi wachisanu ndi chiwiri Aisraeli onse anali atakhazikika mʼmizinda yawo.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13