bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
/
Proverbs 30
Proverbs 30
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
← Chapter 29
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 31 →
1
Nawa mawu a Aguri mwana wa Yake wa ku Masa: Munthuyo anati kwa Itieli, “Inu Mulungu, ine ndatopa. Inu Mulungu, ine ndatopa. Ndalefukiratu.
2
“Ine ndine munthu wopusa kuposa anthu onse; ndilibe nzeru zomvetsa zinthu zonga za munthu.
3
Sindinaphunzire nzeru, ndipo Woyerayo sindimudziwa.
4
Kodi ndani anakwera kumwamba ndi kutsikako? Ndani anafumbatapo mphepo mʼmanja mwake? Ndani anamanga madzi mʼchovala chake? Ndani anakhazikitsa mathero onse a dziko lapansi? Dzina lake ndani? Ndiwuze ngati ukudziwa! Ndipo mwana wake dzina lake ndani?
5
“Mawu ali wonse a Mulungu ndi opanda cholakwika; Iye ndi chishango kwa amene amathawira kwa Iye.
6
Usawonjezepo kanthu pa mawu ake, kuopa kuti Iye angadzakudzudzule ndi kukupeza kuti ndiwe wabodza.”
7
“Inu Yehova, ndikukupemphani zinthu ziwiri musandimane zimenezo ndisanafe:
8
Choyamba, mundichotsere kutali nane mabodza ndi chinyengo. Chachiwiri, ndisakhale mʼmphawi kapena munthu wachuma. Koma muzindidyetsa chakudya chondikwanira tsiku ndi tsiku
9
kuopa kuti ndikakhuta kwambiri ndingayambe kukukanani, nʼkumanena kuti, ‘Yehova ndiye yaninso?’ Kuopanso kuti ndikakhala wosauka ndingayambe kuba, potero nʼkuyipitsa dzina la Mulungu wanga.”
10
“Usamusinjirire wantchito kwa mbuye wake kuopa kuti angakutemberere ndipo iweyo nʼkupezeka wolakwa.”
11
“Alipo ena amene amatemberera abambo awo, ndipo sadalitsa amayi awo.
12
Pali ena amene amadziyesa okha oyera mtima komatu sanachotse zoyipa zawo.
13
Pali ena ndi odzitukumula kwambiri, amene amakweza zikope modzitukumula.
14
Pali ena amene mano awo ali ngati malupanga ndipo zibwano zawo zili ngati mipeni moti amadya amphawi ndi kuwachotsa pa dziko lapansi. Amachotsanso anthu osauka pakati pa anzawo.”
15
“Msundu uli ndi ana aakazi awiri iwo amalira kuti, ‘Tipatseni! Tipatseni!’ ” “Pali zinthu zitatu zimene sizikhuta, zinthu zinayi zimene sizinena kuti, ‘Takhuta!’
16
Manda, mkazi wosabala, nthaka yosakhuta madzi ndiponso moto womangoyakirayakira!”
17
Aliyense amene amanyoza abambo ake, ndi kunyozera kumvera amayi ake, makwangwala a ku chigwa adzamukolowola maso ndipo mphungu zidzadya mnofu wake.
18
Pali zinthu zitatu zimene zimandidabwitsa, zinthu zinayi zimene ine sindizimvetsetsa.
19
Ndipo ndi izi: mmene chiwulukira chiwombankhanga mlengalenga; mmene iyendera njoka pa thanthwe; mmene chiyendera chombo pa nyanja; ndiponso mmene mwamuna achitira akakhala ndi namwali.
20
Umu ndi mʼmene mkazi amachitira atachita chigololo: Atatha kudya ndi kupukuta pakamwa pake iye amanena kuti “Sindinachite kalikonse kolakwa.”
21
Pali zinthu zitatu zimene zimanjenjemeretsa dziko lapansi, pali zinthu zinayi zimene dziko lapansi silingathe kuzipirira:
22
Kapolo amene wasanduka mfumu, chitsiru chimene chakhuta,
23
mkazi wonyozeka akakwatiwa ndiponso wantchito wamkazi akalanda mwamuna wa mbuye wake.
24
Pali zinthu zinayi zingʼonozingʼono pa dziko lapansi, komatu ndi zochenjera kwambiri:
25
Nyerere zili ngati anthu opanda mphamvu, komatu zimasungiratu chakudya chake nthawi ya chilimwe;
26
mbira zili ngati anthu opanda mphamvu komatu zimakonza pokhalapo pawo mʼmiyala;
27
dzombe lilibe mfumu, komatu lonse limakhala mʼmagulumagulu poyenda.
28
Buluzi ungathe kumugwira mʼmanja komatu amapezeka mʼnyumba za mafumu.
29
“Pali zinthu zitatu zimene zimayenda chinyachinya, pali zinthu zinayi zimene zimayenda monyadira:
30
Mkango umene uli wamphamvu kuposa nyama zonse, ndipo suthawa kanthu kalikonse.
31
Tambala woyenda chinyachinya, mbuzi yayimuna, ndiponso mfumu yoyenda pakati pa anthu ake.
32
“Ngati wakhala ukupusa ndi kumadzikweza wekha, kapena ngati wakhala ukukonzekera zoyipa, ndiye khala kaye chete, uganizire bwino!
33
Paja pakutha mkaka mafuta amapangidwa, ndipo ukapsinya mphuno, magazi amatuluka, ndipo mikangano imakhalapo ukalimbikira kukwiya.”
← Chapter 29
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 31 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31