bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 John 1
2 John 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
1
Ine mkulune ndikulemba kalatayi kwa mai wosankhidwa ndi Mulungu, ndi kwa ana ake amene ndimaŵakonda kwenikweni. Ndipo sindine ndekha amene ndimakukondani, komanso onse odziŵa choona.
2
Timakukondani chifukwa cha choona chimene chimakhala mwa ife, ndipo chidzakhala nafe mpaka muyaya.
3
Mulungu Atate ndi Yesu Khristu, Mwana wa Atate, atikomere mtima ndi kutipatsa chifundo ndi mtendere m'choona ndi m'chikondi.
4
Ndidakondwera kwambiri kuti ndidapeza ana anu ena akuyenda motsata choona, monga Atate adatilamulira.
5
Ndiye tsopano ndikukupemphani mai: tizikondana. Pakutero sindikukulemberani lamulo latsopano ai, koma lomwe lija limene takhala nalo kuyambira pa chiyambi.
6
Chikondi chimene ndikunenachi nchakuti tikhale omvera malamulo a Mulungu. Lamulo limene ndikukulemberanilo, monga mudamva kuyambira pa chiyambi, ndi lakuti moyo wanu uzikhala wachikondi.
7
Paja pakuwoneka anthu ambiri onyenga pa dziko lapansi. Iwo savomereza kuti Yesu Khristu adadzakhaladi munthu. Munthu wosavomereza zimenezi ndi wonyenga, ndiponso woukira Khristu.
8
Chenjerani kuti mungataye chimene mwagwirira ntchito, koma yesetsani kuti mukalandire mphotho yathunthu.
9
Aliyense amene sasunga chiphunzitso cha Khristu, koma amaonjezerapo zina, alibe Mulungu. Koma amene amasunga chiphunzitsocho, ameneyo alinso ndi Atate ndi Mwana.
10
Wina aliyense akadza kwa inu osaphunzitsa zimenezi, musamlandire m'nyumba mwanu. Musampatse ndi moni womwe,
11
pakuti wopatsa munthu wotere moni, akuvomereza zochita zake zoipa.
12
Ndili ndi zambiri zoti ndikuuzeni, koma sindifuna kuzilemba m'kalata. Ndikuyembekeza kubwera kwanuko kuti tidzakambirane pakamwa mpakamwa. Pamenepo chimwemwe chathu chidzakhala chathunthu.
13
Ana a mbale wanu wosankhidwa ndi Mulungu akuti moni.
Jump to:
Chapter 1
All chapters:
1