bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
3 John 1
3 John 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
1
Ine mkulune ndikulemba kalatayi kwa Gayo wokondedwa, amene ndimamkonda kwenikweni.
2
Wokondedwa, ndimapemphera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndipo kuti moyo wako wathupi ukhale wolimba, monga momwe uliri moyo wako wauzimu.
3
Ine ndidaakondwa kwambiri pamene abale ena adafika nkumafotokoza za moyo wako m'choona, ndiponso za m'mene umayendera motsata choona.
4
Palibe chondikondweretsa kwambiri koposa kumva kuti ana anga akuyenda m'choona.
5
Wokondedwa, umatsata chikhulupiriro chako pa zonse zimene umachitira abale, makamaka akakhala alendo.
6
Iwo adachitira umboni chikondi chako pamaso pa mpingo. Ndi bwinodi kuti uŵathandize mokondweretsa Mulungu kupitiriza ulendo wao.
7
Paja adaanyamuka ulendo wao chifukwa cha dzina la Khristu, osalandira thandizo kwa akunja.
8
Tsono ife tiyenera kumaŵathandiza anthu otere, kuti tigwirizane nawo pa ntchito yofalitsa choona.
9
Ndidalembera mpingo mau pang'ono, koma Diotrefe safuna kundimvera. Iye amafuna kukhala mtsogoleri.
10
Choncho ndikabwera, ndidzakumbutsa ntchito zimene amachita. Iye amandilalatira ndi mau oipa. Ndipo sachita zokhazi ai, komanso iyeiyeyo amakana kulandira abale, ndipo anthu ofuna kuŵalandira, iye amaŵaletsa, nkumaŵatulutsa mu mpingo.
11
Wokondedwa, usamatsanzire zoipa, koma zabwino. Aliyense wochita zabwino, ndi mwana wa Mulungu, koma wochita zoipa, sadaone Mulungu.
12
Demetrio anthu onse amamchitira umboni wabwino. Ngakhale choona chomwe chimamchitira umboni. Ifenso tikumchitira umboni, ndipo iweyo ukudziŵa kuti umboni wathu ndi woona.
13
Ndinali ndi zambiri zoti ndikuuze, koma sindingakonde kuzilemba m'kalata.
14
Ndikuyembekeza kudzakuwona posachedwa. Pamenepo tidzakambirana pakamwa mpakamwa.
15
Mtendere ukhale nawe. Abwenzi onse akuti moni. Uperekeko moni kwa abwenzi onse mmodzimmodzi.
Jump to:
Chapter 1
All chapters:
1