bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Malachi 4
Malachi 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
1
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Tsiku likubwera pamene anthu onse odzikuza ndi ochita zoipa adzapsa ngati chiputu m'ng'anjo. Tsiku limenelo adzapserereratu osatsalako muzu kapena nthambi. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.
2
Koma inu amene mumaopa dzina langa, dzuŵa lachilungamo lidzakutulukirani lili ndi kuŵala kokuchiritsani. Mudzalumphalumpha mokondwa ngati ana a ng'ombe ochokera m'khola.
3
Tsiku limene ndilikukonzalo mudzapondereza anthu oipa ngati phulusa ku mapazi anu. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.
4
“Kumbukirani zophunzitsa za Mose mtumiki wanga, malamulo ndi malangizo amene ndidamulamula ku phiri la Horebu kuti auze Aisraele onse.
5
“Koma lisanafike tsiku lalikulu loopsalo la Chauta, ndidzakutumizirani mneneri Eliya.
6
Iyeyo adzayanjanitsa atate ndi ana ao, ana ndi atate ao, kuwopa kuti ndingadzabwere kudzatemberera dziko lanu kuti liwonongeke.”
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
All chapters:
1
2
3
4