bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Obadiah 1
Obadiah 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
1
Izi ndi zimene Obadiya adaona m'masomphenya. Naŵa mau a Ambuye Chauta onena za Aedomu. Chauta adatuma wamthenga wake kwa anthu a mitundu yonse, ndipo tidamva mau ake, adati, “Konzekani, tiyeni tikamenyane nkhondo ndi Aedomu.”
2
Chauta akuuza Aedomu kuti, “Ndithu ndidzakutsitsani kotheratu, anthu a mitundu yonse adzakunyozani kwambiri.
3
Mwanyengedwa ndi mtima wanu wonyada. Likulu lanu lili pakati pa matanthwe, mumakhala pa mapiri aatali. Mumanena kuti, ‘Ndani angatitsitse pansi?’
4
Komatu ngakhale muuluke pamwamba ngati chiwombankhanga, ngakhale mumange chisa chanu pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsanibe pansi.” Akutero Chauta.
5
“Akuba akabwera usiku, amangotengako zimene akufuna. Okolola akamathyola zipatso, amasiyako zina. Koma inuyo adani anu akupululani kotheratu.
6
Onani m'mene alisakazira dziko la Esau, ndi m'mene achifunkhira chuma chake chonse.
7
Ogwirizana nanu akunyengani, akupirikitsani m'dziko mwanu. Okuthandizani pa nkhondo akugonjetsani. Abwenzi anu apamtima akutcherani msampha, mwathedwa nzeru tsopano.”
8
Chauta akuti, “Nthaŵi imeneyo ndidzaononga anzeru onse a ku Edomu, ndidzathetsa kuchenjera konse kwa zidzukulu za Esau.
9
Ngwazi za ku Temani zidzachita mantha, ankhondo onse adzaphedwa ku mapiri a Esau.
10
“Aedomu inu, chifukwa cha zankhanza zimene mudachita abale anu, zidzukulu za Yakobe, adzakuchititsani manyazi ndi kukuwonongani mpaka muyaya.
11
Munkangoonerera pamene adani ankaŵalanda chuma chao, munkachita ngati kuvomerezana nawo, amene ankaloŵa pa zipata za Yerusalemu, namagaŵana chumacho.
12
Inu simukadayenera kuŵanyodola abale anu Ayuda chifukwa cha tsoka lao. Simukadayenera kukondwerera kuwonongeka kwao. Simukadayenera kuŵaseka pamene iwo anali m'mavuto.
13
Pa tsiku lao la tsoka simukadayenera kuloŵa mu mzinda wa anthu anga. Pa tsiku lao la tsoka simukadayenera kuŵanyodola. Pa tsiku lao la tsoka simukadayenera kulanda chuma chao.
14
Simukadayenera kudikira pa mphambano za miseu kuti mugwire anthu othaŵa. Pa tsiku lao la tsoka simukadayenera kupereka anthu ao otsala kwa adani.
15
“Posachedwapa lifika tsiku la Chauta pamene Iye adzaweruza mitundu yonse ya anthu. Aedomu inu, adzakuchitani zomwe mudaŵachita ena. Zimene mudachitazo zidzakubwererani.
16
Anthu anga adamwa chikho cha zoŵaŵa pa phiri langa loyera, koma mitundu ina ya anthu idzamwa chikho cha zoŵaŵa kopitirira. Idzachita kugugudiza chikhocho kenaka nkuzimirira pomwepo.
17
“Koma pa phiri la Ziyoni padzakhala ena opulumuka, ndipo phirilo lidzakhala loyera. Pamenepo fuko la Yakobe lidzalandira choloŵa chakechake.
18
Fuko la Yakobe lidzakhala ngati moto, fuko la Yosefe lidzakhala ngati malaŵi a moto, fuko la Esau lidzakhala ngati ziputu. Adzaŵatentha ndi kuŵapsereza, ndipo sipadzapulumuka munthu aliyense.” Akutero Chauta.
19
Ayuda akumwera adzalandira phiri la Esau, akuzambwe adzalandira dziko la Afilisti. Akumpoto adzalandira dziko la Efuremu ndi likulu lake Samariya, ndipo Abenjamini adzalandira dziko lakuvuma la Giliyadi.
20
Aisraele amene anali ku ukapolo adzalandira dziko la Kanani mpaka kumpoto ku Zarefati. A ku Yerusalemu amene anali ku ukapolo ku Sefaradi adzalandira mizinda yakumwera ku Negebu.
21
Ngwazi zochokera ku Yerusalemu zidzagonjetsa ndi kumalamulira dziko la Edomu ndipo ufumu wonse udzakhala wa Chauta.
Jump to:
Chapter 1
All chapters:
1
Recommended Reading
Commentary
Obadiah Commentaries
→
Devotional
Obadiah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→