bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Philemon 1
Philemon 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
1
Ndine, Paulo, amene ndili m'ndende chifukwa cha Khristu Yesu. Ndili limodzi ndi Timoteo, mbale wathu. Tikulembera iwe Filemoni, bwenzi lathu ndi mnzathu wantchito.
2
Kalata yomweyinso tikulembera Afiya, mlongo wathu, ndi Arkipo, msilikali mnzathu pa nkhondo ya Mulungu, ndiponso mpingo wonse umene umasonkhana kunyumba kwanu.
3
Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.
4
Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukira m'mapemphero anga.
5
Pakuti ndikumva kuti umakonda ndi kukhulupirira Ambuye Yesu, ndi oyera onse a Mulungu.
6
Ndimapemphera kuti chikhulupiriro chimene ukugaŵana nawo chigwire ntchito mwamphamvu, kuti udziŵitsitse zabwino zonse zimene timalandira chifukwa cha Khristu.
7
Mbale wanga, chikondi chako chandikondweretsa kwambiri ndi kundithuzitsa mtima, pakuti watsitsimutsa mitima ya oyera onse a Mulungu.
8
Tsono, inde nkotheka kuti ndichite kukulamula m'dzina la Khristu zimene uyenera kuchita.
9
Komabe chifukwa cha chikondi makamaka ndingochita kukupempha, ine Paulo amene ndili nkhalamba, amenenso ndili m'ndende tsopano chifukwa cha Khristu Yesu.
10
Ndikukupempha chifukwa cha mwana wanga mwa Khristu, amene ndidachita ngati kumubala m'ndende muno. Iyeyu ndi Onesimo.
11
Kale unalibe naye ntchito, koma tsopano angathe kutithandiza kwambiri tonsefe, iweyo ndi ine ndemwe.
12
Ndikumtumizanso kwa iwe tsopano, ndipo pakutero ndikuchita ngati kukutumizira mtima wanga womwe.
13
Ndikadakonda kuti akhalebe ndi ine kuno, kuti azinditumikira m'malo mwako, pokhala ndili m'ndende chifukwa cha Uthenga Wabwino.
14
Koma sindikufuna kuchita kanthu osakufunsa, kuwopa kuti ungandichitire chinthu chabwinochi mokakamizidwa, osati mwaufulu.
15
Kapena Onesimo adangokusiya kanthaŵi pang'ono, kuti udzakhale naye nthaŵi zonse,
16
osatinso ngati kapolo, koma kwenikweni ngati mbale wokondedwa. Ine ndimamkonda kwambiri, ndipo iweyo uyenera kumkonda koposa, popeza kuti ndi munthu mnzako ndiponso mkhristu mnzako.
17
Tsono ngati umati ndine bwenzi lako, umlandire iyeyu monga momwe ukadandilandirira ineyo.
18
Ngati adakulakwirapo, kapena ali ndi ngongole kwa iwe, ngongoleyo ikhale yanga.
19
Pano mau aŵa ndikulemba ndi dzanja langalanga kuti, “Ine Paulo ndidzalipira.” Nkosasoŵekera kukukumbutsa kuti paja iweyo ngongole yako kwa ine ndi moyo wako womwe wachikhristuwu!
20
Tsono, mbale wanga, inenso undithandizeko chifukwa cha Ambuye. Undisangulutseko ngati mbale mwa Khristu.
21
Ndikukulembera zimenezi, popeza kuti ndikukhulupirira kuti udzachitadi zimene ndakupempha. Ndikudziŵa kuti udzachita kopitiriranso zimene ndapemphazi.
22
Kanthu kenanso ndi aka: undikonzere malo, chifukwa ndikhulupirira kuti Mulungu adzamvera mapemphero a inu nonse, ndi kundibwezera kwa inu.
23
Akukupatsa moni Epafra, amene ali m'ndende pamodzi nane chifukwa cha Khristu Yesu.
24
Akutinso moni anzanga antchito, Marko, Aristariko, Dema, ndi Luka.
25
Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima nonse.
Jump to:
Chapter 1
All chapters:
1
Recommended Reading
Commentary
Philemon Commentaries
→
Devotional
Philemon Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→