bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Titus 2
Titus 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 3 →
1
Koma iwe uziphunzitsa zogwirizana ndi chiphunzitso choona.
2
Uuze amuna achikulire kuti azikhala osaledzera, ochita zachiukulu, a maganizo anzeru, olimba pa chikhulupiriro, pa chikondi ndi pa kusatepatepa.
3
Chimodzimodzinso azimai achikulire, uŵauze kuti azikhala ndi makhalidwe oyenera azimai oyera mtima. Asakhale osinjirira anzao kapena akapolo a zoledzeretsa. Akhale alangizi abwino,
4
kuti choncho athe kuphunzitsa azimai achitsikana kukonda amuna ao ndi ana ao.
5
Aŵaphunzitse kukhala a maganizo anzeru, opanda dama, osamala bwino zapabanja, ndi omvera amuna ao. Pamenepo anthu sanganyoze mau a Mulungu.
6
Momwemonso amuna achinyamata uŵauzitse kuti akhale odzigwira.
7
Pa zonse iwe wemwe ukhale chitsanzo cha ntchito zabwino. Zophunzitsa zako zikhale zoona, ndipo uziphunzitse mwaulemu.
8
Mau ako akhale oona, kuti anthu asadzathe kuŵatsutsa. Motero wotsutsana nawe adzachita manyazi, atasoŵa kalikonse koipa kuti atinenere.
9
Antchito azimvera ambuye ao, aziŵakondweretsa pa zonse. Asamatsutsana nawo
10
kapena kumaŵabera, koma makamaka adziwonetse kuti ngokhulupirika pa zonse zabwino. Motero pa zochita zao zonse adzaonetsa kukoma kwake kwa zophunzitsa zonena za Mulungu, Mpulumutsi wathu.
11
Mulungutu waonetsa kukoma mtima kwake kofuna kupulumutsa anthu onse.
12
Kukoma mtima kwakeko kumatiphunzitsa kusiya moyo wosalemekeza Mulungu, ndiponso zilakolako za dziko lapansi. Kumatiphunzitsa kuti moyo wathu pansi pano ukhale wodziletsa, wolungama ndi wolemekeza Mulungu.
13
Pajatu tikudikira tsiku lodala, pamene zidzachitike zimene tikuyembekeza, pamene Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu adzaonetsa ulemerero wake.
14
Paja Iye adadzipereka chifukwa cha ife, kuti atipulumutse ku zoipa zathu zonse, ndi kutiyeretsa kuti tikhale anthu ake achangu pa ntchito zonse zabwino.
15
Zimenezi ndizo zimene uyenera kumaphunzitsa. Uziŵalimbikitsa anthu, ndi kuŵadzudzula komwe. Uzichita zimenezi ndi ulamuliro wonse. Wina aliyense asakupeputse ai.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3