Ezekiel 31:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zonsezi zidzatero kuti pasakhale mtengo ndi umodzi womwe wa m'mbali mwa mtsinje umene udzatalike kwambiri, kapena umene nsonga zake zidzafike ku mitambo. Ndiponso pasadzakhale mitengo ina yolandira bwino madzi, imene msinkhu wake ungafike ku mitambo. Pakuti yonseyo kutha kwake ndi kufa, kupita kunsi kwa dziko lapansi, kukakhala pamodzi ndi anthu akufa, amene adaloŵa kale m'manda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti mitengo iliyonse ya kumadzi isadzikuze chifukwa cha msinkhu wao, kapena kufikitsa nsonga zao pakati pa mitambo, ndi kuti amphamvu ao asaime m'kukula kwao, ndiwo onse akumwa madzi; pakuti onsewo aperekedwa kuimfa munsi mwake mwa dziko, pakati pa ana a anthu, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zidzakutero kuti pasakhalenso mitengo inanso ya mʼmbali mwa madzi yotalika kwambiri, imene idzatalike kwambiri ndi songa zake kufika mpaka ku mitambo. Komanso kuti pasadzakhalenso mitengo yolandira bwino madzi, imene idzatalika motero. Paja yonseyo kutha kwake ndi kufa, kupita ku dziko lapansi kukhala ndi anthu akufa amene analowa mʼmanda kale.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti mitengo iri yonse ya kumadzi isadzikuze cifukwa ca msinkhu wao, kapena kufikitsa nsonga zao pakati pa mitambo, ndi kuti amphamvu ao asaime m'kukula kwao, ndiwo onse akumwa madzi; pakuti onsewo aperekedwa ku imfa munsi mwace mwa dziko, pakati pa ana a anthu, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda.