bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
1 Kings 17
1 Kings 17
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 18 →
1
Ndipo Eliya wa ku Tisibe wokhala ku Gileadi ananena ndi Ahabu, nati, Pali Yehova Mulungu wa Israyeli, amene ndimakhala pamaso pace, ngati adzagwa mame kapena mvula zaka izi, koma ntanena ine ndipo.
2
Ndipo mau a Yehova anadza kwa iye, nati,
3
Coka kuno, nutembenukire kum'mawa, ukabisale kumtsinje Keriti uli ku Yordano.
4
Ndipo kudzakhala kuti uzikamwa mumtsinje, ndipo ndalamulira makungubwi kukudyetsa kumeneko.
5
Momwemo iye anamuka, nacita monga mwa mau a Yehova, nakakhala kumtsinje Keriti uli ku Yordano.
6
Ndipo makungubwi anamtengera mkate ndi nyama m'mawa, ndi mkate ndi nyama madzulo; namamwa iye mumtsinje.
7
Ndipo kunacitika, atapita masiku ena mtsinje udaphwa, popeza munalibe mvula m'dziko.
8
Ndipo mau a Yehova anadza kwa iye, nati,
9
Nyamuka, pita ku Zarefati wa ku Zidoni, nukhale kumeneko; taona, ndamlamulira mkazi wamasiye wa kumeneko akudyetse.
10
Tsono iye ananyamuka namka ku Zarefati, nafika ku cipata ca mudzi; ndipo taona mkazi wamasiye anali kutola nkhuni; ndipo iye anamuitana, nati, Unditengere madzi pang'ono m'cikho, ndimwe.
11
Ndipo m'mene analikumuka kukatenga iye anamuitananso, nati, Unditengerenso kanthongo ka mkate m'dzanja lako.
12
Nati iye, Pali Yehova Mulungu wako, ndiribe mkate, koma kaufa dzanja limodzi kali m'mbiya, ndi mafuta pang'ono m'nsupa; ndipo taona, ndirikutola nkhuni ziwiri kuti ndikadziphikire odekha ndi mwana wanga, tidye, tife.
13
Ndipo Eliya anati kwa iye, Usacita mantha, kacite monga umo wanenamo, koma thanga wandiocerako kamkate, nubwere nako kwa ine; ndipo utatero udziphikire wekha ndi mwana wako.
14
Popeza atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Mbiya ya ufa siidzatha, ndipo nsupa ya mafuta siidzacepa, kufikira tsiku lakugwetsa mvula Yehova pa dziko lapansi.
15
Ndipo iye anakacita monga mwa mau a Eliya, nadya iye mwini, ndi iyeyo, ndi a m'nyumba ace, masiku ambiri.
16
Mbiya ya ufa siidatha, ndi nsupa ya mafuta siinacepa, monga mwa mau a Yehova amene ananenetsa Eliya.
17
Ndipo kunali, zitatha izi, mwana wa mkazi mwini nyumbayo anadwala; ndipo pokula nthenda yace, analeka kupuma.
18
Ndipo mkaziyo ananena ndi Eliya, Ndiri nawe ciani munthu iwe wa Mulungu? Kodi wadza kwa ine kundikumbutsa chimo langa, ndi kundiphera mwana wanga?
19
Ndipo ananena naye, Ndipatse mwana wako. Namtenga m'mfukato mwace napita naye ku cipinda cosanja cogonamo iyeyo; namgoneka pa kama wa iye mwini.
20
Napfuulira kwa Yehova, nati, Yehova Mulungu wanga, kodi mwamgwetsera coipa mkazi wamasiye amene ndikhala naye, kumphera mwanace?
21
Nafungatira katatu pa mwanayo, napfuulira kwa Yehova, nati, Yehova Mulungu wanga, ndikupemphanf, ubwere moyo wace wa mwanayu m'cifuwa mwace.
22
Ndipo Yehova anamvamau a Eliya, ndipo moyo wa mwanayo unalowanso mwa iye, nakhalanso moyo.
23
Ndipo Eliya ananyamula mwanayo, natsika naye ku cipinda cosanja, nalowa naye m'nyumba, nampereka kwa amace; nati Eliya, Taona, mwana wako ali moyo.
24
Ndipo mkazi anati kwa Eliya, Ndizindikira tsopano kuti ndinu munthu wa Mulungu, ndi kuti mau a Yehova ali m'kamwa mwanuwo ngoona.
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22