bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
1 Kings 5
1 Kings 5
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 6 →
1
Ndipo Hiramu mfumu ya ku Turo anatuma anyamata ace kwa Solomo, popeza anamva kuti adamdzoza mfumu m'malo mwa atate wace; pakuti Hiramu adakondana ndi Davide masiku onse.
2
Ndipo Solomo anatumiza mau kwa Hiramu, nati,
3
Mudziwa inu kuti atate wanga Davide sanathe kumangira dzina la Yehova Mulungu wace nyumba, cifukwa ca nkhondo zakumzinga konseko, mpaka atawaika Yehova pansi pa mapazi ace.
4
Koma tsopano Yehova Mulungu wanga wandipumulitsa ku mbali zonse; palibe wotsutsana nane, kapena coipa condigwera.
5
Ndipo taonani, ndikuti ndimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, monga Yehova anauza atate wanga Davide, ndi kuti, Mwana wako ndidzamuika pa mpando wako wacifumu m'malo mwako, iyeyo adzamangira dzina langa nyumbayo.
6
Ndipo tsono, lamulirani kuti anditemere mitengo yamkungudza ku Lebano, ndipo akapolo anga adzakhala ndi akapolo anu, ndipo ndidzakupatsani mphotho ya akapolo anu monga mudzanena; popeza mudziwa kuti pakati pa ife palibe mmisiri wakudziwa kutema mitengo ngati anthu a ku Sidoni.
7
Ndipo kunacitika, pamene Hiramu anamva mau ace a Solomo, anakondwera kwakukuru, nati, Alemekezeke Yehova lero amene wampatsa Davide mwana wanzeru akhale mfumu ya anthu aunyinji amenewa.
8
Ndipo Hiramu anatumiza kwa Solomo, nati, Ndazimva zija munatumiza kwa inezo, ndidzacita cifuniro canu conse, kunena za mitengo yamkungudza ndi mitengo yamlombwa.
9
Akapolo anga adzatsika nayo ku Lebano kufika nayo ku nyanja yamcere, ndipo ine ndidzaiyandamitsa paphaka kufikira komwe mudzandiuzako, ndi kumeneko ndidzaimasula, ndipo mudzaitenga; nimudzacita cifuniro canga, kumapatsa banja langa zakudya.
10
Tsono Hiramu anapatsa Solomo mitengo yamkungudza ndi mitengo yamlombwa monga momwe anafuniramo.
11
Ndipo Solomo anapatsa Hiramu miyeso ya tirigu zikwi makumi awiri ndiyo zakudya za banja lace, ndi miyeso makumi awiri ya mafuta oyera; motero Solomo anapatsa Hiramu caka ndi caka.
12
Ndipo Yehova anapatsa Solomo nzeru monga momwe adamlonjezera; ndipo panali mtendere pakati pa Hiramu ndi Solomo, iwo awiri napangana pamodzi.
13
Ndipo mfumu Solomo anasonkhetsa athangata mwa Aisrayeli onse, ndi athangatawo ndiwo anthu zikwi makumi atatu.
14
Ndipo anawatuma ku Lebano mwezi umodzi zikwi khumi kuwasintha, mwezi umodzi iwo anali ku Lebano, miyezi iwiri anali kwao; ndipo Adoniramu anali kapitao wa athangata.
15
Ndipo Solomo anawasenzetsa akatundu anthu zikwi makumi asanu ndi awiri, ndi anthu zikwi makumi asanu ndi atatu anatema m'mapiri;
16
osawerenga akapitao a Solomo akuyang'anira nchito, ndiwo zikwi zitatu mphambu mazana atatu, amenewo analamulira anthu aja akugwira nchito.
17
Ndipo mfumu inalamula iwo, natuta miyala yaikuru-ikuru ya mtengo wapatali, kuika maziko ace a nyumbayo ndi miyala yosemasema.
18
Ndipo omanga nyumba a Solomo ndi omanga nyumba a Hiramu ndi anthu a ku Gebala anaisema, naikonza mitengo ndi miyala yakumangira nyumbayo.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22