bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
2 Kings 20
2 Kings 20
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 21 →
1
Masiku ajawo Hezekiya anadwala, nafuna kufa. Namdzera Yesaya mneneri mwana wa Amozi, nanena naye, Atero Yehova, Siyira banja lako; pakuti udzafa, sudzakhala ndi moyo.
2
Pamenepo anatembenuzira nkhope yace kukhoma, napemphera kwa Yehova, ndi kuti,
3
Mukumbukile Yehova kuti ndinayendabe pamaso panu m'coonadi, ndi mtima wangwiro, ndi kucita zokoma m'kuona kwanu. Nalira Hezekiya kulira kwakukuru.
4
Ndipo kunali, asanaturukire Yesaya m'kati mwa mudzi, anamdzera mau a Yehova, ndi kuti,
5
Bwerera, nunene kwa Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga, Atero Yehova Mulungu wa Davide kholo lako, Ndamva pemphero lako, ndapenya misozi yako; taona, nelidzakuciritsa, tsiku lacitatu udzakwera kumka ku nyumba ya Yehova.
6
Ndipo ndakuonjezera pa masiku ako zaka khumi ndi zisanu; ndidzakupulumutsa iwe ndi mudzi uno m'dzanja la mfumu ya Asuri; ndidzacinjiriza mudzi uno, cifukwa ca Ine ndekha, ndi cifukwa ca Davide mtumiki wanga.
7
Nati Yesaya, Tenga ncinci yankhuyu. Naitenga, naiika papfundo, nacira iye.
8
Nati Hezekiya kwa Yesaya, Cizindikilo cace nciani kuti Yehova adzandiciza, ndi kuti ndidzakwera kumka ku nyumba ya Yehova tsiku lacitatu?
9
Nati Yesaya, Cizindikilo ndici akupatsa Yehova, kuti Yehova adzacicita conena iye; kodi mthunzi umuke m'tsogolo makwerero khumi, kapena ubwerere m'mbuyo makwerero khumi?
10
Nati Hezekiya, Kutsikira mthunzi makwerero khumi nkopepuka, kutero ai; koma mthunzi ubwerere makwerero khumi.
11
Napfuulirakwa Yehova Yesayamneneriyo, nabweza iye mthunzi m'mbuyo makwerero khumi, ndiwo amene udatsikira pa makwerero a Ahazi.
12
Nthawi ija Berodaki Baladani mwana wa Baladani mfumu ya Sabulo anatumiza akalata ndi mtulo kwa Hezekiya, popeza adamva kuti adadwala Hezekiya.
13
Ndipo Hezekiya anawamvera, nawaonetsa nyumba yonse ya cuma cace, siliva, ndi golidi, ndi zonunkhira, ndi mafuta okometsetsa, ndi nyumba ya zida zace, ndi zonse zopezeka pacuma pace; panalibe kanthu m'nyumba mwace, kapena m'ufumu wace wonse osawaonetsa Hezekiya.
14
Koma Yesaya mneneri anadza kwa mfumu Hezekiya, nati kwa iye, Anatani anthu awa? anadza kwa inu kufumira kuti? Nati Hezekiya, Afumira dziko la kutari ku Babulo.
15
Nati iye, Anaona ciani m'nyumba mwanu? Nati Hezekiya, Zonse za m'nyumba mwanga anaziona, palibe kanthu pacuma canga kosawaonetsa.
16
Ndipo Yesaya anati kwa Hezekiya, Tamverani mau a Yehova.
17
Taonani, akudza masiku kuti zonse za m'nyumba mwako, ndi zokundika makolo ako mpaka lero, zidzatengedwa kumka ku Babulo, kosasiyidwa kanthu konse, ati Yehova.
18
Nadzatenga ena a ana ako oturuka mwa iwe, amene udzawabala, nadzakhala iwo adindo m'cinyumba ca mfumu ya Babulo.
19
Pamenepo Hezekiya anati kwa Yesaya, Mau a Yehova udawanena ndi abwino. Natinso, Si momwemo nanga, mtendere ndi coonaeli zikakhala masiku anga?
20
Macitidwe ena tsono a Hezekiya, ndi mphamvu yace yonse, ndi umo anamangira dziwe ndi mcera, nautengera mudzi madzi, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?
21
Nagona Hezekiya ndi makolo ace; nakhala mfumu m'malo mwace Manase mwana wace.
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25